ZITSANZO ZA MMENE TINGAYANKHIRE MAFUNSO A ANA OKHUDZA CHIKHULUPIRIRO

01 KUKHULUPIRIRA MWA ALLAH
01 MAFUNSO OKHUDZA KUKHULUPIRIRA MWA ALLAH
02 MAFUNSO OKHUDZA ANGELO
03 MAFUNSO OKHUDZA MABUKU
04 MAFUNSO OKHUDZA ATUMIKI
05 MAFUNSO OKHUDZA KUKHULUPILIRA TSIKU LOMALIZA
06 MAFUNSO OKHUDZA KUKHULUPILIRA CHIKHONZERO CHA MULUNGU

Ndithu mayankho omwe abwera mu gawo ili choyambirira akulunjika kwa makolo ndi aliyense yemwe amakhala akuyankha mafunso a ana , monga aphunzitsi , alangizi , oyanganira maphunziro ndi onse oyanjanitsa anthu, amenewa tikuwapempha kuti awasanje ndi kuwaumba mayankho amenewa molingana ndi misinkhu, maphunziro ndi kuthekera kwa nzeru za mwanayo, chifukwa ife sitingakwanitse kuika yankho limodzi loyenera ana a misinkhu yonse yosiyana siyana pa zaka, nzeru ndi kuthekera , pachifukwa ichi, chimene chimakhala chofunikira kwa ife ndi yankho lenilenilo osati mau a yankho wo ayi (125), komanso tikuyenera kumasinthasintha kayankhulidwe ka yankholo pakati pa kuyankha mwachindunji ndi mopanda chindunji; ndi cholinga choti tipereke mlingo waukulu wa chithunzithunzi kwa wowerenga, ndipo iye malinga ndi udindo ndi ntchito yake atenga chenicheni cha mayankho amenewa nabwereza kasanjidwe ndi kaumbidwe kake molingana ndi njira yomwe ili yoyenera ndiyapamwamba komanso yabwino kwambiri kwa mwana wake.

Ndipo pofuna kuyankha mafunso a mwana okhudza chikhulupiriro, makolo akuyenera kukhala ndi mlingo wokwanira wa maphunziro a chipembedzo wowaloleza iwo kupereka matanthauzo oyambirira omwe angawafotokozere ana awo zinthu zobisika mwa njira yolingana ndi nzeru ndi kuthekera kwa anawo, ndipo zovuta zomwe a zamaphunziro amakumana nazo si kusonkhanitsa maphunziro kokha ayi, koma kuwaika (maphunzirowo) mukakhalidwe koti nzeru za anawo zithe kuwalandira ndi kuwamvetsetsa, komanso kuwabweretsa moyenera ndi nthawi komanso ndi nyengo yomwe mwanayo amakhala.

Ndipo zikubwerazi ndi zina mwa zitsanzo za mafunso omwe amabwerabwera pa lilime la ana, ndipo dziwani kuti awa simafunso onse ayi, koma ofunikira kwambiri mwa iwo ndiponso omwe amafunsidwafunsidwa kwambiri, ndipo tayesetsa kuika mayankho abwino kwambiri okha okha malinga ndi kuona kwathu, ndipo sitikudzichemerera kuti amenewa ndi mayankho apamwamba kwambiri ayi; koma kuti izo ndi zitsanzo zoti makolo atha kuzitenga ngati poyambira, ndipo tikukutsimikizirani kuti mayankho amenewa mutha kuwakonza, kuwapungula kapena kuwaonjezera.

CHENJEZO: Yemwe angaganize kuti iye sangakwanitse kuphunzitsa ana ake, kuopera kukumana ndi mafunso ovuta; ndiye kuti iyeyo ndi wolakwitsa, khalidwe limenelo ( lokonda kufunsa mafunso ovuta) kwa ana ndi chizindikiro cha thanzi lawo kuti akukula mwa chilengedwe komanso kuti nzeru ndi kuthekera kwa kuganizira kwawo kukukula mwa dongosolo, ndi kuti pakapezeka vuto, ndiye kuti ndi chifukwa cha kulephera makolo kukwaniritsa makulidwe a mwana wawo ndi kulephera kutsegula ngodya za nzeru zake ndi kulandira kwake zinthu zobisika ndi zooneka zomwe zamuzungulira (126). Choncho makolo ndi aliyense yemwe amayanganira mwana adzayenera kulimbikira kumpatsa mwanayo mayankho ogwira mtima olo kangachepe, chifukwa yankho logwira mtima pang’ono limathandiza kudekhetsa mtima wake, maganizo ake ndi kukhala kwake ndi anthu, pomwe mayankho olakwika amaonjezera mwana kubalalika, ndipo kubalalika kumeneku kumapangitsa kusokonekera kwa khalidwe la mwanayo, ndi kuperewera kuganiza kwake komanso kachitidwe kake ka zinthu.

Ndithu mavuto akulu akulu samadza nthawi imodzi, olo moto umayamba ndi lawi lalingono, choncho; makhalidwe ambiri oyipa pa munthu amaoneka ngati njere yayingono yothiriridwa ndi kuzengereza ndi kuimikira imikira, ndipo kamakulirakulira kamba ka kusalabada chifukwa chotengeka ndi umoyo mpaka kukula namerera mizu mu mtima moti siingatheke kuchoka kapena kuzulidwa (127).

MAFUNSO OKHUDZA

KUKHULUPIRIRA MWA ALLAH

Ndithu mafunso omwe amakonda kuzungulira kwambiri mmutu wa mwana akakhala wachichepere kwambiri ndiwo mafunsa okhudza Allah. Ndipo pano tibweretsa ambiri mwa mafunso amenewa omwe ana amakonda kufunsa kwa makolo awo:

Funso

Kodi Allah (MULUNGU) ndi ndani

Choyamba, tisadikire kuti mpakana mwana atifunse zokhudza Allah,koma timufotokozere mwachangu za Allah nthawi zonse komanso pa zochitika ndi pampata (opportunity), ndithu yankho lolondola la funso la mwana lokhudza Allah ndi mbiri zake lidzamanga maziko a Tauheed( umodzi wa Allah) ndi kukhulupirira Allah ( mwini ulemelero wonse) mu nzeru za mwana komanso mu mtima wake,pachifukwa chimenechi, ndithu njira ya pamwamba kwambiri ndiko kuzipanga nzeru za mwana kuti zisiye kuganiza za maonekedwe a Allah mwini wakeyo koma aziganiza za mitendere ndi kudabwitsika kwa chilengedwe zomwe Allah walenga zomwe zikusonyeza kuti Allah alipo, monga kumwamba ndi thambo,nyenyezi, dzuwa ,mwezi,nyanja ,mitengo, ndi zina zotero (128),

Werengani zambiri

Kodi Allah (MULUNGU) ndi ndani?

ndikumudziwitsa ma ubwino a Allah pomulenga iye ndikumulengeranso ziwalo, monga :maso, makutu,pakamwa , lilime,mikono, miyendo ndi ziwalo zake zina. Ndipo timuuze kuti mitambo imeneyi anailenga ndi Allah, chimodzimodzinso nthaka, mitengo yonse, ndi zina zotero, kufikira mwana atazolowera ndikusangalatsidwa nawo mawu amenewa, ndipo akamatifunsa kuti kodi Allah ndi ndani? Tizimuyankha mwa chidule kuti iye (Allah) ndi amene adalenga anthu ndi zinthu zonse zomwe zatizungulira, kenako timupatse zitsanzo zochuluka pa chimenechi.

Tikamaliza kumudziwitsa ndi kumuonetsa zolengedwa za kumwamba ndi za pansi pano, namudziwitsa dongosolo ndi kasanjidwe ka ukatswiri ka zinthu zimenezi, tidzamuuze mwanayo kuti: kodi waliwona dongosolo la kasanjidwe kameneka, ndithu yemwe anapanga zimenezi ndi Allah, ndithu tikatero iye adzamudziwa mbuye wake mozindikira ndi mwa maumboni. Timuuzenso kuti Allah ndi amene analenga chilichonse ndipo iye (Allah ) safanana ndi chilichonse, ndipo iye ndi wachifundo, wodyetsa ndi wopereka, komanso ali ndi maina ndi mbiri zabwino ndi za pamwamba zokha zokha, choncho iye akuyenera kupembedzedwa ndipo asaphatikizidwe ndi china chilichonse, komanso timuuze kuti Allah amakonda kwambiri ana moti anawalamula akuluakulu kuti azithandiza , kuyanganira ndikuchitira ubwino ana ndi anthu onse,ndipo iye akatiwerengera pa ntchito zomwe tagwira zabwino ndi zoipa zomwe potilipira sawab (zabwino) kapena chilango, moti iye ndi amene amamulipira munthu wochita zabwino molingana ndi ubwino wake, komanso woipitsa molingana ndi kuipitsa kwake. Ndipo ndi bwino kuwaphunzitsa anawo ma Surah (ndime za mu Korani zazifupizifupi; chifukwa masurah amenewa ali ndi mayankho abwino abwino okhudza Allah ndi mbiri zake, moti iye ndi Allah yemwe: sanabereke kapena kuberekedwa, ndipo alibe wofanana naye (129).

Nzothekanso kumufunsa funso loti: “kodi ndi ndani yemwe anakugulira zovala zokongola zimenezi?”Ndipo iye adzayankha kuti: “bambo anga”, nanga ndi ndani yemwe amakuperekeza popita ku sukulu? Iye adzayankha kuti bambo anga, nanga ukadwala ndani amene amakuperekeza kwa dotolo? Iye adzati bambo anga, nanga ndi ndani yemwe amakutenga kupita kokasangalala nthawi ya tchuthi? Iye adzati bambo anga, nde kuti bambo ako ndi amene amakupangira zonse? Iye adzati: inde.

Zikatero muuzeni mwanayo kuti tsono Allah ndi amene amatiyang’anira tonsefe (iweyo, ife kuphatikizanso bambo akowo), iye ndi amene analenga chilichonse, zonse zomwe umaziona mmbali mwako ndi zolengedwa ndi Allah, dzuwa ndi mwezi, mitambo, Nyanja ndi mapiri, kulenga anthu,zinyama ndi mbalame, kulenga angelo ndi ziwanda,Allah ndi amene analenga dziko lonseli, ndipo Allah ndi wopereka komanso wachifundo, amatiyanganira ndi kutisamalira, amatikonda ndi kumatibweretsera maubwino nthawi zonse.

Funso

Kodi Allah amafanana ndi munthu Him

Ayi safanana naye,iye safanana ndi chilichonse, iye ndi amene analenga ine, iweyo ndi anthu onse, analenga mitengo, mitsinje,Nyanja ndichina chilichonse pa dziko lapansi pano, kwa iye ndi kumene kumachokera mphamvu za pamwamba , akafuna china chake amangochiuza kuti: ”chitika” ndipo chimachitikadi. ndipo Allah ndiwosiyaniratu ndi munthu, munthu sangathe kulenga munthu nzake, koma Allah zimenezo amakwanitsa, ndipo angathe kupanga chilichonse chomwe wafuna, nde chifukwa cha kuti palibe amene angathe kumuona Allah pa umoyo uno wa dziko la pansi, palibe amene angamufotokoze Allah (maonekedwe ake), ife sitingakwanitse kumuona Allah (chifukwa iye) ndi dangalira lamphamvu, kuthekera kwa maso athu ndi koperewera.

Werengani zambiri

Kodi Allah amafanana ndi munthu?

kenako timpemphe mwanayo kuti apite akayang’ane ku ma dangalira (rays) adzuwa ndipo asakasinzine ayi, kenako timufunse kuti: kodi ungakwanitse kuyang’ana (china chake) ku dzuwako? Ndipo iye adzatsutsa, choncho tidzamuuza kuti: mwana wanga wolemekezeka, dziwa kuti dangalira lochokera kwa Allah sitingathe kukwanitsa kupilira kuliyang’ana, koma tikakalowa ku Jannah tikamuona Allah muchilolezo chake.

Pamenepa mwana atha kukutsutsa ndi kuonetsa kusakhutitsidwa ponena kuti: zimatheka bwanji Allah yo osafanana ndi chilichonse? Apa pazafunika kumuuza mogwira mtima koma modekha ponena kuti: ndithu nzeru zathu ngakhale zitakhala zazikulu ndi zomvetsetsa kwambiri chotani,zidzakhalabe nzeru za umunthu ndizosakwanira, zimadziwa zokhazo zomwe Allah anafuna kuti zidziwe, ndipo zomwe Allah sanafune kuti nzeru zathu zidziwe sizingadziwe, moti nzosatheka kuti tidziwe zinthu zonse, chifukwa tidzakhalabe anthu. Timuuzenso kuti: Allah akanakhala munthu ngati ife nde kuti bwenzi akumadwala monga mmene ife timachitira, bwezinso akumadya, kumwa ndi kumwalira ngati mmene anthu amachitira, koma Allah samapanga nawo kapena kumuchitikira chilichonse mwa zimenezi, iye ndi wopezeka nthawi zonse, ndipo iye ndi mlengi wa mitambo, nthaka ndi chilichonse chimene chili pa dziko pano, choncho Allah safanana ndi chilichonse.

Tingathenso kumufunsa mwanayo kuti: kodi ifeyo anthu tingathe kuchiuza chinthu kuti “chitika!” nachitikadi? Mwana adzayankha kuti ayi, zikatero ife limodzi ndi mwanayo tidzatulutsa ganizo loti: ndithudi Allah simunthu ngati ife ayi koma iye ndi mlengi wamkulu kwambiri. Timuuzenso kuti kumva kwathu kuli ndi malire, timangomva zokhazo zimene zikupezeka pa mtunda wina wake, tikanakhala kuti timamva china chilichonse tikanatopa, maso athunso ndi ofooka, timangoona zokhazo zimene zili pa mtunda wina wake, ife sitingathe kuona zomwe zili kuseli kwa chipupa – mwachitsanzo-, ndiye mmene kulili kumva ndi kuona kwathu kuti ndi kofooka, chimodzimodzinso nzeru zathu ndi zofooka chifukwa sizimazindikira zinthu zonse (zimangozindikira zinthu zochepa zokha).

Ndithu nzeru za munthu ndi zofooka, moti kuyambira pamene Allah adalenga munthu kufikira lero, gawo la zimene munthu samazidziwa limakhala lalikulu kwambiri kuposa gawo la zomwe amazidziwa, ngakhale nzimu womwe umapezeka mthupi la munthu ameneyu –mwachitsanzo – ngakhale tili nawo pafupi kwambiri, koma sitimaudziwa kwenikweni kapena kuuyerekeza ndi china chake,ngati izi zikuchitikira pa chomwe chili mwa ife, kuli bwanji za chomwe chili kunja kwa ife?, kotero, ndithu nzeru za munthu zidzakhala zofooka , sizingathe kudziwa mmene Allah amaonekera; kotero maonekedwe a Allah sungawadziwe kudzera mu zithunzi kapena , nzeru ndi kuganizira chabe ayi, koma kudzera mu malamulo a Allah okha tingathe kudziwa,Quru’an yanenetsa zimenezi motere: “ Palibe chilichonse chofanan ndi iye, iye ndi wakumva zonse komanso amaona zonse”. (Surat Ash Shura: 11).

Kuchokera pa mawu amenewa, tikupeza kuti ndithu Allah safanana ndi ifekapena chilichonse (130), zimenezi zikusonyeza kuti Allah ndi wamkulu kwambiri yemwe tikuyenera kumukonda, kumupempha komanso kumuopa, ndipo ukulu umenewu ukukwanira kupangitsa kuti kukamuona iye ku Jannah kukakhale chonyaditsa chapamwamba kwambiri mu Jannah yonse.

Funso

Kodi yemwe adamUlenga Allah ndi ndani

Zikadakhala kuti alipo yemwe adalenga Allah,inenso nkadafunsa kuti: ndani adalenga mlengi? Sichoncho? Kotero tikuyenera kudziwa kuti zina mwa mbiri za mlengi ndi zakuti: iye sadachite kulengedwa ndipo iye ndi amene adalenga zolengedwa zonse, akadakhala kuti iye adachita kulengedwa sitikadamupembedza kapena kutsatira chiphunzitsondi malamulo ake, ndiye funso lonena kuti ndani adamulenga Allah silolondola ndipo lilibe tanthauza, mwachitsanzo, mmodzi wa iwo atakufunsa kutalika kwa nzere wachinayi wa chinthu cha mizere itatu (triangle)? palibe choyankha pamenepo chifukwa triangle ili ndi mizere itatu yokha, nde pamene pakulakwika mu funso loti analenga Allah ndi ndani? Ndi liwu loti: “adamulenga” lo motsogozedwa ndi liwu loti: “Allah”lo, chifukwa mawu amenewo sangayendere limodzi ayi, chifukwa wopembedzedwa salengedwa, ndipo ntchito yolengedwa ndithudi imakhala pa zolengedwa pokha, palibe amene angakwanitse kumulenga Allah, akadapezeka ameneyo nde kuti Allah nayenso akadakhala cholengedwa, koma Mulugu ndi wopezeka nthawi zonse, alibe chiyambi ngakhalenso mathero.

Werengani zambiri

Kodi yemwe adamUlenga Allah ndi ndani?

Olo titayesera kuika mtsutso woti kuli mlengi wa Allah(wapamwambamwamba), ndiye kuti anthu azingofunsana funso lomweli loti adalenga mlengi ndani? Choncho lizingopitilira osafika pa mathero a mtsutsowo, zosatheka kupezeka mlengi wa mlengi, ndipo pofuna kuyandikitsa zedi titenga chitsanzo cha msilikali ndi chipolopolo, iye akafuna kuombera azipemha chilolezo kwa nzake yemwe ali kumbuyo kwake, nayenso kuti apereke chilolezo akuyenera kupempha chilolezocho kuchokera kwa amene ali kumbuyo kwake, ndikumayenda choncho mpaka kopanda polekezera, funso nkumati: kodi msilikali uja adzaombera? Yankho nkumati: ayi, chifukwa sadzapeza msilikali yemwe adzapereke chilolezo choti iye awombere, pomwe tcheni chija ngati chingafike pa munthu yemwe pamwamba pake palibenso wina woti angapereke chilolezo chowombera ndiye kuti adzaombera, koma kupanda kupezeka munthu ameneyu, ndiye kuti anthuwo olo atachuluka motani chipolopolo chimenecho sichidzaombedwa, iwo adzakhala ngati ma ziro (zero) ukawandanditsa, olo atachuluka mopanda mapeto, iwo adzakhalabe opanda nambala ya chilendo(adzakhalabe ziro), pokha pokha kutaikidwa kumayambiriro kwakeko nambala ina yosiyana ndi ziro, monga (1) ndi manambala ena (131).

Funso

KODI ALLAH ADACHOKERA KUTI NANGA ALI NDI ZAKA ZINGATI?Kodi Allah asanapezeke kunali ndani

Ngati iwe - m’bale wanga wolemekezeka – ukudziwa kuti Allah sadalengedwe; ndithudi chimodzimodzi iye sadabeleke kapena kubelekedwa, alibenso chiyambi ngakhalenso mathero, kotero alibe zaka zakubadwa ngati momwe zikhalira kwa ife anthu, chifukwa Allah ndiye mlengi wamkulu wolemera kwambiri, mwini mphamvu komanso wolimba, mwini ulemerero ndi wachifundo yemwe ali ndi maina abwino okhaokha ndi mbiri zabwino komanso zokwanira osati zopunguka, Allah ndi amene anapezeketsa dzikoli ndi zolengedwa zonse.

Werengani zambiri

KODI ALLAH ADACHOKERA KUTI NANGA ALI NDI ZAKA ZINGATI? Kodi Allah asanapezeke kunali ndani?

Funso limeneli ndi chimodzimodzi ndi lija lonena kuti adamulenga Allah ndi ndani, ili ndi funso lolakwika chifukwa Allah ndi woyambirira ndipo pasanapezeke Allah panalibe chilichonse, komanso iye ndiwomaliza pambuyo pake palibe chilichonse, Allah akunena kuti (132)“ Iye alibe chiyambi, wamuyaya, woonekera, wobisika kwambiri (saoneka) ndipo iye ndi wodziwa chilichonse” Surat: Al Hadid: 3)ndithu nthawi ili ngati malo sizingaike malire a Allah, ndipo nthawi ndi chimodzi mwa zolengedwa za Allah, kotero zolengedwa sizingaike malile kapena kumuzungulira mlengi wake, Allah ali ndi mbiri zonse zabwino ndi zokwanira, apa tikuyenera kuchenjera ndikulandira langizo (wasiyyah) la mtumiki (SAW) lomwe Abu Hurairah adamumva mtumiki akunena kuti: “Satana amatha kumufikira mmodzi wa inu ndikumamufunsa kuti kodi ndani adalenga chakuti? Nanga chakuti anachilenga ndi ndani? Mpaka amafika pofunsa kuti: ndani analenga mbuye wako? Pakafika pamenepa, iye adzitchinjirize mwa Allah kenako aziiwale (zomwe amafunsidwa ndi satanazo)” (Bukhar 3276), kudzitchinjiriza mwa Allah ndi kutembenuzira maganizo amwana ku zinthu zina mosakhala mwachindunjiku, ndicholinga choti asapitirize mafunso amenewa, nakonso ndi umodzi mwa mitundu yakuyankha kofunikira pa nkhani imeneyi, pomwe kutembenuzamaganizo a mwana ndi kuwatalikitsa ku zimenezi si kuti ndi chifukwa choti ulibe yankho ayi, koma kutseka molowera manong’onong’o a satana

Funso

Kodi Allah ndi wamwamuna kapena wankazi

Tikuyenera kuzitalikitsa nzeru za mwana kuti zisamaganizire kwambiri za maonekedwe a Allah, ndipo tiziongolere nzeru zake kuti ziziganizira zinthu zomwe zingamubweretsere phindu, apa tsopano zidzakhala bwino kumuuza momveka kuti kukhala mwamuna kapena mkazi ndi zinthu zosiyanitsira magulu ndi mitundu ya zolengedwa za moyo, izi ndi zina mwa zomwe Allah anazipatsa zolengedwa zake, Allah akunena kuti: “ Ndipo iye ndi amene adalenga mitundu iwri: chachimuna ndi chachikazi”. (Surat Al Nnajim: 45) pomwe Allah ali pamwamba pa onsewo.
komanso kuli zolengedwa zina zomwe sizimalowa nawo mmagulu amenewa, monga: angelo, kumwamba, mitambo, mphepo ndi madzi, zimenezi sizimatchedwa zazimuna kapena zazikazi, choncho ngati zikutheka kupezeka zolengedwa zina zosalowa nawo mmagulu amenewa, nde kuti Allah ndi amene akuyenera kwambiri kusapezeka nawo mmagulu amennewa: “Palibe chilichonse chofanana ndi iye, iye ndi wakumva zonse ndiponso woona zonse” (Surat Shura: 11).

Funso

KODI NCHIFUKWA CHIYANI TIMAKHULUPIRIRA KUTI ALLAh ALIPO? NANGA TINGATSIMIKIZE BWANJI ZIMENEZI

Kukhulupirira mwa Allah ndi chibadwa cha munthu wina aliyense chimene palibe yemwe angachitsutse ndipo ma umboni oti Allah alipo ndi ochuluka zedi, ndipo anthu adakatulukirabe ma umboni pamwamba pa maumboni ena, wina aliyense mwa anthuwo molingana ndi mbali yake ya maphunziro imene akufufuza, ndipo umboni wa chibawa cha munthu umatsimikizira kuti Allah alipo, Allah akunena kuti: “Dzikakamize wekha kuchilengedwe chimene (Allah) adalengera anthu,( ichi ndi chipembedzo cha chisilamu chomwe nchoyenerana ndi chilengedwe cha Munthu)”. (Surat Al Rum: 30) tonsefe timamva mumtima mwathu kuti muli mphamvu ina yake yomwe imauuza mtimawo za ukulu, mphamvu ndi chisamaliro cha Allah pa ife, pomwe maumboni okhudzika ochokera mmaphunziro akutsimikiziranso kuti pa dziko pano pali dongosolo la kuya ndi la mtengo wapatali, ndipo dongosolo limeneli pali amene analiika; chifukwa zolengedwa zonsezi ndi ndani anazipezeketsa?

Werengani zambiri

KODI NCHIFUKWA CHIYANI TIMAKHULUPIRIRA KUTI ALLAh ALIPO? NANGA TINGATSIMIKIZE BWANJI ZIMENEZI?

Kutheka kuti zinangopezeka mwangozi popanda wozipezeketsa,ngati zili choncho nde kuti palibe angadziwe mmene zinapezekera zinthu zimenezi, chimenecho ndi chiyembekezo choyamba.Pomwe chiyembekezo chachiwiri ndi choti: zinthu zimenezi zinadzipezeketsa zokha ndipo zimadziyang’anira zokha,ndipo chiyembekezo chachitatu ndi chakuti: pali amene anazipezeketsa ndi kuzilenga.

Ndiye tikayang’ana ziyembekezo zitatu zonsezo, tipeza kuti chiyembekezo choyamba ndi chachiwiricho nzosatheka, zikatero nde kuti choyambacho ndi chimene chingakhale choona komanso chomveka, zoti pali mlengi yemwe adazilenga(Allah),ndipo izi ndi zomwe Allah adazinena mu Qur’ani ponena kuti: “ Kapena adalengedwa popanda Mlengi kapena iwo adadzilenga okha, kodi iwo ndi amene adalenga thambo ndi nthaka? Koma iwo sakhulupilira kweni kweni”. (Surat Al Tur: 35 -36).

Ndipo ena mwa maumboni osonyeza kuti Allah alipo ndi izi: kuyankha kwa Allah ma dua(mapempho)a anthu, ukatswiri wa kalengedwe ka mitambo ndi nthaka, Allah akunena kuti: “Ndithudi mukalengedwe kakumwamba ndi dziko lapansi ndikusinthana kwausiku ndi usana, ndizisonyezo(zoti kuli mlengi wa zimenezi) kwa eni nzeru”. (Surat Al Imran: 190), komanso poona ukadaulo wa kalengedwe ka munthu, Allah akunena kut: “Ndimwainu nomwe kodi simuona?”.(Surat Adhariyat: 21). Ndi kalengedwe ka nyenyezi, mapiri, zinyama, ndi zina zotero, zonsezo zimasonyeza ukatswiri wa Mulungu pa zolenga zake.

Ndithu zizindikiro zoti Mulungu alipo zili pali ponse: pa dzikoli, m’mitima kapena mmatupi (a anthu ndi zinyama), ndizipatso zonse zikusonyeza kuti kuli Mu-lungu m’modzi wayekha (yemwe adazipezeketsa zonsezi) ndipo kupezeka kwa zolengedwa zonsezi kukusonyeza kuti kuli ndi cholinga chapamwamba zedi chomwe Mulungu adazilengera ndipo zonsezo zimapembedza Mulungu (Allah) yekha yemwe alibe chophatikizana nacho (133).

Ndizothekanso kumusimbira mwanayo nkhani ya Abu Hanifah (R.a) atamupempha anthu ake kuti awatsimikizire zoti kuli Tauhid ya Rububiyyah (zoti Mulungu yekha ndi amene amalenga ndi kumasamalira zomwe walengazo) Abu Hanifah anati kwa anthuwo tisanakambe nkhani imeneyi tandiuzeni zachombo chomwe chimadziyendetsa chokha pa mtsinje wa Dijlah (Tigris) nichikatenga chakudya ndi katundu wina pachokha nabweleraso pachokha, ndikumaimanso chokha kenako ndi kutsitsa katunduyo chokha ndikumabwelera, zonsezo chombocho chimapanga chokha popanda wochiyendetsa komanso wochiyang’anira (Tandiuzeni kuti zimatheka bwanji zimenezi?) ndipo iwo adati zimenezo sizingatheke komanso sizidzatheka mpaka kalekale, Abu Hanifah adat: ngati sizingatheke zimenezo pa Chombo; kuli bwanji dziko lonseli m’mene lakuliramu kuyambira kumwamba mpaka pansi pano! (134) Ndithu nzosatheka kuti kalengedwe kaluso kadziko limeneli kakhale kopanda Mlengi wakutha kwambiri komanso wozindikira zedi.

Nzothekanso kumufunsa mwana kuti kodi ukamamva kupweteka m’mimba siuja umazindikira kuti uli ndi njala, kenako ndikumafunafuna chakudya wekha wekha kuti uthetse njalayo? Komanso ukamva ludzu siuja iwe umafunafuna chakumwa chimenechingathetse ludzu limeneli?ndipo ukanunkhitsa fungo labwino siuja umasangalatsidwa nalo iwe? pomwe ukamva fungo loipa siuja umanyasidwa? Komanso ukamaona maluwa, mitambo ndi chilengedwe chomwe chatizungulira, kodi simumasangalatsidwa nacho ndi kukupatsa chimwemwe?
Chimodzimodzi m’bale wanga wolemekezeka tonsefe timazindikira mwaife tokha kuti timafunikira wachikulire kwambiri kuti tizimudalira nthawi iliyonse tikafuna kuti tipeze mpumulo ndi chitetezo, chifukwanthawi imeneyi timayamba kubanika ndi kudandaula; ndithudi mwaife tokha mwachidziwikireni kuti timathawira kwa Mulungu ndikumupempha iye, ndipo tikakhala pa mtendere timamutamanda iye pa mtendere umeneu.

Funso

Kodi Mulungu amamva, kuona kapena kulankhula ngati ife

Ndithu Mulungu amalankhula, kumva komanso kuona, Mulungu akunena kuti: “Ndithu Mulungu wamva mau a (mkazi) akubwezerana bwezerana nawe(mau) pazamwamuna wake” (Surat Al mujadilah: 1). adanenaso kuti: “Mulungu adati musaope ndithu ine ndili nanu pamodzi ndikumva ndiponso ndikuona” (Surat twaha: 46) adatiso: “Ndithu iye (Mulungu) akuona zonse zimene muchita” (Surat Hudu: 112), koma singati m’mene ife timalankhulira kapena kumvera ndikuonera ayi, chifukwa Mulungu ndiwosiyana ndi zolengedwa zake, iye amamva mau ngakhale atakhala mauwo alankhulidwa mobisika chotani, amaona chilichonse angakhale chitatalikira motani, Mulungu amaona ndi kumva chilichonse koma kuona ndi kumva kwakeko sikumafanana ndi kumva kapena kuona kwa zolengedwa zake chifukwa kuona ndikumva kwa zolengedwa ndi kofooka komanso kopunguka chifukwa Mulungu akulankhula Kunena kuti: “Palibe chilichonse chofanana ndi iye, iye ndiwakumva zonse komanso woona zones”. (Surat Ashura: 11).
Ndipo ndibwino kuzilumikiza zimenezi ndi khalidwe la chindunji, monga kufunsa kuti: ngati Mulungu ali wakumva ndi kuona mwamphamvu, kodi tikuyenera kukamba zomwe sizingamusangalatse ndiye atione tili pakaonekedwe komwe iye samakafuna?! (135).

Funso

Kodi Mulungu samva njala kapena ludzu

Mulungu (mwini mphamvu ndi ulemelero wonse) ali ndi mbiri zokwanira zokha zokha ndipo alibe mbiri iliyonse yopunguka. Ndithu njala ndi ludzu ndi zizindikiro zakufooka ndipo sizifunikira kumpatsa Mulungu, komanso Mulungu safuna chakudya kapena chakumwa (136); chifukwa Mulungu ndi amene analenga chilichonse kotero safunikiranso chilichonse mwazimenezo, kotero iye akanafunikira chinthu china chake sakanakhala Mulungu. Inde Mulungu ndi chikhomo samadya komanso safunikira chakudya ndi chakumwa, iye alibe nazo ntchito zimenezo, komanso iye ndi amene amapemphedwa ndi zolengedwa kuti azithandize, monga kuzidyetsa, kuzimwetsa ndi kuzipangira zokhumba zake.

Werengani zambiri

Kodi Mulungu samva njala kapena ludzu?

Ndizothekanso kumuuza mwanayo kuti: ndithudi Mulungu palibe chomuyerekezera ndi zolengedwa zake, ndipo sizoona kuti chilichonse chomwe ife tingapange ndi kuchitulukira chingakhale mbiri yathu kapena maonekedwe anthu ayi, si choncho? Mulungu samamva njala kapena ludzu, ndilorenindikufunseni funso: kodi amene amapanga njinga ndi ndani? Iye adzayankha kuti “kampani yopanga njinga”; zilibwino kwambiri, tabwera mwana wanga tilingalire limodzi kuti njinga izimufunsa yemwe anaipanga kuti: umadya chiyani? Umamwa chiyani? Ungayiyankhe chiyani? Ndingaiuze kuti zimenezo sizikukukhudza, upin-dula chiyani ukadziwamo, kodi yankho lako lizaonjezera chiyani ku ntchito yake yeniyeni yanjinga yoyenda mwachangu ndi mopanda ulesi, chabwino (zilibwino kwambiri), chimodzimodzi –mwana wanga – Mulungu anatilengera ntchito yochepa ngatim’mene Allah akunenera: “Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti azindipembedza” (surat adhariat: 56). Choncho mafunso amenewa sangatithandize kupeza ntchito ina yoonjera pantchito yomwe Mulungu anatilengera, koma mmalo mwake mafunso amenewa atisokoneza nzeru zathu kuti tisathe kugwira ntchito yomwe adatilengera. Kodi nanga njingayi idzalunjika liti kwa ifeyo kutipempha thandizo? Ikazaonongeka china chake, ndithu iyo idzalunjika kwa okonza kuti akakonze choonongekacho, chimodzimodzi ife timalunjika kwa Mulungu pomupempha tikaona kuperewera pakupembedza kwathu, kapena likatigwera vuto lina lake.

Funso

Kodi mphamvu za Mulungu ndi zochuluka bwanji

Ndithu ife tikamanena zamphamvu kapena kuthekera komwe kuli koperewera; ndiye kuti tikutanthauza mbiri yofooka, chifukwa pothera mphamvu imeneyo ndipamene padzayambire kufooka, ndipo kufooka sikumakhala pa Mulungu choncho kuthekera kwa Mulungu ndikopanda malire ndipo palibe chomwe chingamufoole iye kapena kumulepheletsa, Mulungu akunena kuti: “Kodi siukudziwa kuti Mulungu ngokhonza chinthu chilichonse” (surat bakara: 106) ndipo akafuna chithu amangoti “chichitike” ndipo chimachitika.
Mulungu ndi wakutha chilichonse; chifukwa iye ndi Mlengi wachili chonse, sichingamukanike chili chonse chadziko lapansi ndi kumwamba komwe.

Pomwe kuthekera kokhala ndi malire ndikwa zolengedwa, chifukwa kumeneko ndikuthekera kochita kulengedwa. Pomwe kuthekera kwa Mlengi; kulibe malire kapena kupunguka. Choncho; Mulungu yekha ndi amene akuyenera kupembedzedwa ndi kupemphedwa; chifukwa iye yekha ndi amene ali ndi kuthekera koyankha ndikuthandiza zofuna zazolengedwa, kuwadyetsa ndikuwakwanilitsira zofuna zawo komanso kuyendetsa zichitochito zawo (137).

Funso

Kodi Mulungu amakhala kuti nanga ndi wamkulu motani

Pambuyo poti mwana wamvetsa pansi pansi zoti Mulungu ndi amene adamulenga komanso kuti Mulungu amakonda ana kwambiri, ndikuti iye anamupatsa mwanayo mitendere yochuluka, ndizotheka nthawi imeneyo kumulongosolera kuti Mulungu alipo ndipo amapezeka kumwamba, Mulungu akunena kuti: “Kodi muli m’chitetezo kwa amene ufumu wake uli kumwamba” (Surat al muluku: 16), iye ( Mulungu) alikumwamba koma kuzindikira kwake kuli paliponse, Mulungu akunena kuti: “Ndipo iye alinanu paliponse pamene muli” (Surat Al Hadid: 4), ndipo si zoyenera kwa ife Kunena kuti Mulungu ali pali ponse ayichifukwa kutero zizatanthauza kuti Mulungu ali mkati mwachili chonse, zimenezo sizoona ayi; ndithu ife timagwiritsitsa zomwe zili muchiphunzitso, Mtumiki (saw) anamufunsapo kapolo wachikazi kuti: “Kodi Mulungu amakhala kuti?” iye adati: “kumwamba”, Mtumiki (saw) adati “nanga ndine yani?” iye adati: “Mthenga wa Mulungu”, Mtumiki adati: “Mmasuleni ukapolo chifukwa iye ndi wokhulupirira”. ( Muslim -537).

Werengani zambiri

Kodi Mulungu amakhala kuti nanga ndi wamkulu motani?

Ndiye ngakhale iye amakhala kumwamba komabe amakwanitsa kutiona ndikutimva malo ali onse, ndipo timutsimikizire mwanayo nthawi zonse kuti Mulungu amamuona iye nthawi zonse, umeretse chimenechi mu mtima wamwana ndipo chikhale chomulondera iye (mlonda wake), pomwe zokhudza kukula kwake: Mulungu wapamwamba mwamba asafanizidwe ndi cholengedwa chilichonse, chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa chili chonse, kuposa zolengedwa zonse moti pakapezeka zolengedwa zazikulu zikulu ndithu Mlengi wake ndi wamkulu kuposa izo; ndipo iye ndi amene adzazule mapiri, ndi kugwedeza Nyanja, amawalamula madzi kuti azilowa munthaka, ndipo zonse zomwe zimachitika padziko pano zimachitika muchilamulo chake ndi chifuniro chake, ndithu Mlengi safuna thandizo lochokera kuzolengedwa zake, thambo ndichimodzi mwa zolengedwa za Mulungu ndipo kupezeka kwake (Allah) sikuti kwagona pa kupezeka kwa thamboko ayi, ndipo iye sapeza phindu lililonse kuchokera ku thambolo, chifukwa Mulungu ndi wolemera kwambiri kuposa wina aliyense ndipo safuna thandizo la chilichonse (138).

Funso

KODI ZIMATHEKA BWANJI IFE ALLAH AMATIONA POMWE IFE IYE SITIMAMUONA

Ndithu maso omwe Mulungu anatipatsa pa dziko lapansi pano ndi ofooka sangathe kuona zochuluka; pa chifukwa ichi mudzaona munthu akugwiritsa ntchito zipangizo zoonera zinthuzazing’onozing’ono (microscope) ndi zipangizo zina zokulitsira zinthu, ndiye ngati munthu akulephera kuziona zinthu zolengedwa, kusamuona Mulungu kudzakhala koposa,ndithu kuthekera kwa munthu pa dziko la pansi lino sikungamuthandize kuti amuone Mulungu,ife sitingakwanitse kumuona Mulungu koma timamukhulupirira, timakhulupiriranso kuti Mulungu ndi wachifundo komanso amatikonda, ndiwamphamvu komanso ali ndikuthekera kopanga chilichonse, ndipo amadziwa chilichonse, ndiponso akudziwa kuti ife pa nthawi ino tikukambirana za iye,ndithu Mulungu safanana nafe kutalitali, choncho iye amationa tonsefe nthawi imodzi ngati mmene zimakhalira munthu akakwera pamwamba pa nyumba yosanjikizana amatha kumawaona anthu onse omwe ali munsewu pomwe iwo samamuona iye,choncho Mulungu amationa koma ife sitimamuona iye.

Werengani zambiri

KODI ZIMATHEKA BWANJI IFE ALLAH AMATIONA POMWE IFE IYE SITIMAMUONA?

Ndithu pali zinthu zambiri zomwe sitingathe kuziona koma izo zilipo, ndipo timuuze mwana kuti: ndithu maso athuwa sangathe kuona zinthu zonse ayi, ife sitimatha kuwaona mawu ngakhale timawamva, sitingaone mphepo ngakhale imatikhudza (imatiomba), ndiye maso athuwa sangathe kumuona Mulungu pa dziko pano, koma ku Jannah – mu chifuniro cha Mulungu- tikakhala kumeneko ndi maso abwino kwambiri omwe akakwanitse kumuona Mulungu wapamwambamwamba, choncho Mulungu akulankhula kunena kuti: “Maso samufika iye (samuona); koma iye amawafika maso (amawaona pamodzi eni masowo). Iye ngodziwa zobisika kwambiri ndi zoonekera”. (Al ani’am:103).

Funso

KODI ALLAH AMAKWANITSA BWANJI KUWAONA ANTHU ONSE KUMACHITA KUTI IWO NDI OCHULUKA KWAMBIRI

Kuti tithe kuliyankha funso limeneli, timutenge mwanayo tikaime naye pa msewu, numufunsa kuti: uziwayang’ana anthuwo kenako undiuze kuti waona angati, tiwerenge limodzi anthu omwe ungawaonewo, kenako tikwere pa nyumba yaitali ndikumuuzanso kuti aziwerenga omwe akuwaona, kenako tikwere naye nyumba yaitali kwambiri ndikumuuzanso kuti aziwerenga anthu omwe akuwaona, kenako timupatse magalasi kuti azitha kuwaona anthuwo ndi kuwawerenga bwinobwino.

Werengani zambiri

KODI ALLAH AMAKWANITSA BWANJI KUWAONA ANTHU ONSE KUMACHITA KUTI IWO NDI OCHULUKA KWAMBIRI?

Kudzera mu chitsanzo chimenechi, tidzatha kumuwalitsira mwanayo kuti ndithudi ife sitingathe kuyeza bwino zinthu patokha pogwriritsa ntchito miyezo ya umunthu wathu, choncho timufotokozere iye kuti kuthekera kwa Mulungu ndi kwa kukulu kwambiri kuposa kuthekera kwa zolengewa zake zonse,ndipo tiike mu nzeru za mwanayo nthawi zonse mawu awa: “Kodi siukudziwa kuti Mulungu ngokwanitsa kupanga chinthu chilichonse”. (Baqarah :106).

Tingathenso kumufunsa funso lokhudzika ili: kodi umakhulupilira kuti nyerere zimationa ife m’mene tilili kapena zimangotiyerekeza kapena zimangoona zithunzi? Iye adzayankha kuti nyerere imangokwanitsa kuona mbali chabe yaying’ono kwambiri yachala chathu chachikulu chakumiyendo, mwinanso ingathe kuganizira kuti chalacho ndi phiri kwa iyo. Chabwino, nanga ukuganiza kuti nyerere ingathe kufunsa kuti umakwanitsa bwanji kutiona ife tonse pakamodzi? Yankho lako lidzakhala lonena kuti: zimenezo ndi zachikhalire: chifukwa zikugwirizana ndi kuthekera kwako komwe Mulungu anakulengera.

Nyerere kuthekera kwake ndi kochepera, ndipo patha kupezeka nyumba zochuluka za nyerere m’malo osiyana siyana padzenje limodzi, ndipo nzophweka kwa iwe kuwaona malo onsewa nthawi imodzi, pomwe nyerere ndikuthekera kwake kochepa kuja siingathe kuona momwe iwe ungaonere, ndiye monga m’mene tagwirizanira kale kuti Mulungu safanana ndi china chilichonse, komanso kuti iye amatha chilichonse, choncho sizoyenera kumufunsa Mulungu ndikuthekera kwathu kochepaku zinthu zoti kwa iye ndizosakaikitsa, chifukwa kuthekera kwa Mulungu ndi kwakukulu kwambiri kuposa kuthekera kwa zolengedwa zonse, chifukwa Mulungu akunena kuti: “Kodi sukudziwa kuti Mulungu ngokhonza (ngokwanitsa) chinthu chilichonse” (Surat AlBakara: 106).

Funso

Kodi Mulungu amawaonanso anthu ndimum’dimamomwe? KODI ALLAH AMAKWANITSA BWANJI KUTIONA TIKAKHALA MNYUMBA ZATHU, MAKOMO NDI MAWINDO ALI OTSEKEDWA

Tingathe kumupatsa mwana filimu kuti aonere makamaka mwa ma filimu omwe amaonetsa asilikali a pamtunda omwe amaona pogwiritsa ntchito ma galasi oyang’anira ukafika usiku,ndipo timuonetsenso ma filimu oonetsa zina mwa zinyama ndi mbalame zomwe zimaona usiku, komanso ena mwa ma filimu omwe amaonera ndi masewero omwe amasewera mumatha kupezeka zipangizo zojambulira monga (laser) zomwe zimaonetsa za kuseli kwa zinthu komanso zimationetsa zinthu zomwe zili mu mdima, pambuyo pake timuuze mwanayo kuti:ukumuona munthu (cholengedwa) wofooka mmene akumakwanitsira kuona mu mdima nthawi zina? Kuli bwanji mbuye wathu amene anamulenga munthu ameneyu ndi zolengedwa zonse (139), ngati Mulungu anatipatsa kuthekera kopanga zachilendo zimenezi, kodi angalephere- iye amene ali wakutha ndi woyang’anira – kupanga zimenezo? Kumachita kuti ndi wakutha komanso wamkulu kwambiri, ndipo kuthekera kwa Mulungu palibe amene angakutchinge kapena kukulepheretsa.

Werengani zambiri

Kodi Mulungu amawaonanso anthu ndimum’dimamomwe? KODI ALLAH AMAKWANITSA BWANJI KUTIONA TIKAKHALA MNYUMBA ZATHU, MAKOMO NDI MAWINDO ALI OTSEKEDWA?

Timuonetse mwana zithunzi zakuchipatala kenako timufotokozere kuti ndithu munthu yemwe Mulungu adamulenga adakwanitsa kuliona fupa litatsekedwa bwino bwino pogwiritsa ntchito chipangizo cha x-ray, kuli bwanji Mbuye wathu yemwe adalenga munthuyo? Ndithudi Mulungu amationa tikakhala m’manyumba mwathu titadzitsekera makomo onse , ndithu Mulungu safanana ndi chili chonse, iye salingati munthu yemwe zipupa zimamulepheretsa kuona, Mulengi sangakhale ngati cholengedwa; chifukwa Mulungu ndiwakutha chilichonse, ndipo ndizoyenera kulilumikiza yankho limeneli ndi zichito chito zamwanayo polimbiktsa mbali yakuzilondera ndikuchimva kukoma chipembedzo mu mtima mwake mwanayo (140).

Funso

KODI ALLAH AMADZIWA BWANJI NTCHITO ZATHU? NANGA AMAKWANITSA BWANJI KUYANG’ANIRA ANTHU ONSE

Mwana akuyenera kudziwa nthawi zonse kuti Mulungu ali ndi mbiri zabwino ndizokwanira zokha zokha, adziwenso kuti kuthekera kwa Mulungu kulibe malire, iye ndi wakutha zedi, Mulungu akunena kuti: “Kodi sukudziwa kuti Mulungu ngokhonza (ngokwanitsa) chinthu chilichonse?” (Surat Al Bakara: 106), ndiye chifukwa chakuti Mulungu ali ndi kuthekera kwa kukulu palibe chimene chimamukanika padziko lapansi pano ndi kumwamba komwe, ndizosatheka kuyerekeza kuthekera kwa Mulungu ndi kuthekera kwa zolengedwa, kuthekera kwazolengedwa ngakhale kungakule bwanji, kuthekera kwa Mulungu kudzakhala koposa kwambiri. Pofuna kuyandikitsa tanthauzo limeneli: nzotheka kumpatsa chitsanzo chazojambulira video (video camera) m’mene chimakwanilitsira kujambula ndikusunga kakang’ono ndikakakulu kena kalikonse komwe diso lake (camera) laona, ndipo Mulungu ali ndi kuthekera kwakukulu kwambiri koposa chilichonse, iye amatha kuyang’anira anthu onse nthawi imodzi, chifukwa kuthekera kwake kulibe malire, ndipo Mulungu amadziwa ndipo kudziwa kwake ndi kokwanira komanso kopanda malire pa china chilichonse (141).

Tithanso kumupatsa chitsanzo ichi: tiyerekeze kuti pali kampani yayikulu ukufuna uziyang’anira ogwira ntchito mmenemo, ndipo mwawayikira ma kamera iwo asakudziwa, ndipo mwayamba kuwayang’anira mwachinsinsi kudzera pa ma sikilini (sreen/video monitor) oonetsa kalikonse kochitika pa kampaniyo nthawi imodzi, ngati kapolo kapena cholengedwa chofooka chomwe Mulungu adachilenga chikukwanitsa kupanga zimenezo, ndiye akalephere yemwe adalenga kapolo ameneyo ndicholengedwa chimenechi kuwaona akapolo ake onse nthawi imodzi?.

Funso

Kodi Nchifukwa chiyani munthu amamwalira ndipo Mulungu samwalira? KODI ALLAH AMANDIKONDA NGATI MMENE INE NDIMAMUKONDERA

Ndithu infa ndi chikonzero cha Mulungu chomwe anakonzera zolengedwa zake Mulungu akunena kuti: “Chamoyo chilichonse chidzalawa infa,kenako mudzabwezedwa kwa ife”. (Al Akabut: 57), ndiye kufa kwa munthu ndichiyambi cha moyo uli nkudza, ndipo umenewo ndiwo moyo umene uli wofunikira kwambiri.

Ndithu infa ndi chizindikiro chosonyeza kufooka chomwe wamoyo wolengedwa aliyense chidzamupeze, ndiye kufooka sikumapezeka mwa mulungu, chifukwa Mulungu sadalengedwe ndipo sadzamwalira, pomwe munthu ndiwolengedwa ndipo amamwalira, ndithu umoyo wa Mulungu sufanana ndiumoyo waife, umoyo waife umatha ndi ifa, ndipo zolengedwa zonse zidzamwalira, adzatsale ndi Mulungu yekha, ndithu moyo wa Mulungu ndiwokwanira ndipo ukuyenera kukhala ndi mbiri zonse zakukwanira, makamaka mbiri yoti iye ndiwa moyo yemwe sadzafa (142).

Werengani zambiri

Kodi Nchifukwa chiyani munthu amamwalira ndipo Mulungu samwalira? KODI ALLAH AMANDIKONDA NGATI MMENE INE NDIMAMUKONDERA?

Mulungu ndi wokhululuka ndi wachifundo amawakonda anthu abwino okhazikika ndi onena zoona, Mulungu akunena kuti: “Allah awakonda iwo, nawonso amukonda Allah yo” (surat Al Maida: 54), ndipo zizindikiro zachikondi cha Mulungu pakapolo wake ndi izi: Mulungu amawalemekeza iwo ndikuwachengetera, ndikuwayendetsera zichito chito zawo, kuwadyetsa ndi kuwakhululukira, ndipo aliyense amachikhudza chifundo cha Mulungu ndi ulemelero womwe Mulungu anamupatsa, ndipo Mulungu amamukonda kapolo wake yemwe amamumvera iye ndikudziyandikitsa kwa iye ndipo amagwiritsa ntchito mphamvu yake yonse kuonetsa chikondi kwa Mulungu; monga kusamala swala, kuchitila ubwino makolo, kupereka chaulere, kuchitira ubwino anthu, kunena zoona, kuwerenga Quru’an, kumutchulatchula Mulungu, ndi ntchito zina zabwino, yemwe angapange zimenezi Mulungu wapamwamba mwamba amamukonda.

MAFUNSO

OKHUDZA ANGELO

Iwo ndi zina mwa zolengedwa za Mulungu analengedwa kuchokera kudangalira (kuwala), Mulungu adawalenga iwo asadamulenge munthu. Iwo ali ndi chifuniro, nzeru ndi mapiko, ndipo maonekedwe a nkhope zawo ndi okongola, alinso ndikuthekera kodzisintha kuti aoneke ngati munthu, iwo samadya kapena kumwa, iwo ndi akapolo a Mulungu amapanga zomwe alamulidwa, iwo ali ndi maulemelero a pamwamba osiyanasiyana.
Ndipo wolemekezeka kwambiri mwaiwo ndi Jibir (as); iye ndi amene anapatsidwa ntchito yokafikitsa chivumbulutso (uthenga wa Mulungu) kwa atumiki.
Wina ndi Mikail;Israfil ndi ena otero, ena mwaiwo ndi amene anapatsidwa ntchito yosamalira akapolo a Mulungu nthawi ina iliyonse, ndipo pali chiwerengero chochuluka cha angelo, mngelo wina aliyense ali ndi ntchito yakeyake yomwe Mulungu anamupatsa kuti azigwira (144).

Ndithu angelo alipo ochuluka kwambiri, palibe amene amadziwa kuchuluka kwawo kupatula Mulungu (mwini ulemero wapamwamba), ena mwa maina awo ndi awa: Jibiril, Mikail, Israfiil, Ridhwani, Maliki (as), palinso omwe anyamula mpando wa Mulungu, ena otetezera akapolo a Mulungu, ndi ena omwe amasunga ntchito za akapolo a Mulungu, ndi ena otero (145).

Mulungu analenga angelo kuti azigwira ntchito yabwino, iwo onse ndi abwino nthawi zonse, sapanga choipa ndipo sachidziwa. Angelo kwao kweni kweni ndi kumwamba, koma kutsika kwa munthu kubwera pansi pano kunapangitsa kuti angelo ena azitsikanso pansi pano kudzagwira ntchito zawo zina zomwe Mulungu wawalamula kuti adzagwire, monga kudzawasamalira, ndikudzawatetezera ndi kuwayang’anira anthu, ndi kudzafikitsa uthenga kwa aneneri, ndikudzapulumutsa, ndikuwapemphelera chikhululuko anthu, kudzakhala nawo anthu pamalo pomwe akumutchula Mulungu ndi ntchito zina zotero.
Ndipo ndi zotheka kumuuza mwana kuti angelo ali ndi ntchito ziwiri zikulu zikulu zofunikira kwambiri izi: kupembedza Mulungu ndikuyika ndondomeko yakayendetsedwe kadziko limeneli.

Anthu alibe kuthekera kowaona angelo mkaonekedwe kao komwe Mulungu adawalegera. Nchifukwa chake iwo amadzisintha namaoneka ngati munthu ndicholinga choti anthu athe kuwaona iwo kapena kugwira nawo ntchito, ngati m’mene Jibiril anadzisinthila naoneka ngati munthu wachimidzi midzi pa nkhani yophunzitsa malamulo achipembedzo ija (147).

Izi ndizina mwa zolengedwa za Mulungu, Mulungu adazilenga izi kuchokera kumoto, ndipo iwo analengedwera kuti azimvera malamulo a Mulungu ndikusiya zomwe waletsa, iwo amamwalira ngati m’mene zolengedwa zonse zimamwalilira, ife sitingakwanitse kuziona ndipo tilibe kuthekera kotero, Mulungu adawalengera iwo kuthekera kosiyana ndi kuthekera kwa munthu, iwo amatha kuuluka ndi kuyenda mwachangu komanso amakwanitsa kudzisintha maonekedwe (kusanduka) (148), ndipo kalengedwe kawo ndikosiyana ndi kamunthu, chifukwa munthu adalengedwa kuchokera kudothi pomwe ziwanda zinalengedwa kuchokera kumoto.

Ndithu angelo kalengedwe kawo ndikopitilira samwalira kufikira tsiku lomwe lidzaimbidwe lipenga, pomwe ziwanda zimamwalira zisanafike tsiku limeneli. Kotero angelo ndi amene amachotsa mizimu kudzera muchilolezo cha Mulungu akagamula kuti wina wake amwalire “Mulungu ndiyemwe amatenga mizimu pa nthawi ya ifa yake” (surat zumar: 42), choncho angelo ndi amphamvu kwambiri kumbali imeneyi ndi paumoyo wadziko lapansiwu, ndipo satana ndi abale ake amaopa angelo, monga m’mene zinachitikira tsiku la nkhondo ya Badri satana ataona angelo omwe Mulungu adawatumiza kuti akawathandizire anthu okhulupilira, iye anawauza makafiri kuti: “Ine ndikuzipatula mwainu, Ndithu ine ndikuona zomwe inu simukuziona, ndithu ine ndikuopa Mulungu, ndiponso Mulungu ngwaukali polanga” (surat Al Anifaal:48).

Nzoona kuti angelo ndi zina mwazolengedwa za Mulungu, ndipo chilichonse chidzaoonongeka ndipo angelo adzamwalira kupatula Mulungu wapamwamba mwamba, chifukwa iye ndi wamoyo wampakana kalekale (150), Mulungu akunena kuti: “chinthu chilichonse chidzaonongeka kupatula nkhope yake (Mulunguyo)”, ( surat Al Qasas: 88), ndiye zonse zili padziko lapansi pano zidzamwalira, chimodzi modzinso zonse zomwe zili kumwamba zidzamwalira kupatula omwe Mulungu adzawafune kuti nthawi imeneyo asamwalire, ndipo palibe yemwe adzatsale osamwalira kupatula Mulungu wapamwamba mwamba, chifukwa iye ndiwamoyo yemwe sadzamwalira mpaka kale kale (wamuyaya).

MAFUNSO

OKHUDZA MABUKU

Awa ndi mabuku omwe Mulungu adawavumbulutsa kwa atumiki ake (madalitso ndi mtendere a Mulungu zipite kwaiwo); ndi cholinga choti afalitse uthenga ndi kulamulira malamulo ali mmenemo, mabuku amenewa ndi chiongoko komansochifundo kwa zolengedwa zonse ndi cholinga choti zisangalale pa dziko lino lapansi ndi moyo womwe uli nkudza.
Ndipo zomwe tikudziwa zokhuda mabuku amenewa ndi zoti: Mulungu adabvumbulutsa kwa mneneri Ibrahim (Abraham) (a.s.) buku lotchedwa (Suhufu), kwa Daud (Davide) zaburi (masalimo), kwa Musa (Mose) Taurat {chipangano cha kale}), ndipo kwa Issa mwana wa mariam (Yesu) Injeel {chipangano chatsopano}), ndipo kwa Muhammad (Quru’an) (151).

Ngati chipangizo chophweka chopangidwa ndi munthu chimafunikira ka buku kotidziwitsa mmene chipangizocho tingachigwiritsire nthito moyenera; ndiye kuti munthu – yemwe ndi chopangidwa (cholengedwa) ndi Mulungu- azafunikira kwambiri buku lomuongolera ndikumudziwitsa njira yachiongoko,kupambana ndi kulongosoka padziko la pansi ndi dziko lomwe lili nkudza, Mulungu akunena kuti: “Kodi asadziwe yemwe adalenga (zinthu zomwe adalenga)? Kumachita kuti iye ngodziwa zinthu zing’onozing’ono kwambiri ndiponso wodziwa nkhani zonse”. (surat Almulk: 14).

Komanso Quru’an ndi chodabwitsa; chifukwa mtumiki Muhammad (saw) ndi mneneri womaliza wa aneneri onse, choncho pakuyenera kuti chodabwitsa chake chikhale chopitilira mpaka kalekale, chifukwa palibeso mneneri wina pambuyo pake, ndiye pakuyenera kuti umboni ukhalepobe nthawi zonse, pakuyenera kuti tchalenji yake ikhalebe kufikira tsiku lachiweruzo.
Ndipo maumboni osonyeza kuzizwitsa kwa Qur’an ndi ochuluka zedi, ofunikira kwambiri mwaiwo ndi awa:
kuzizwitsa kwake pachilankhulo ndi kulongosoledwa bwino kwa mfundo zake, ndipo ichi ndichimene Mulungu anawatchalenja nacho aluya omwe anali otsogola pakulongosola ndikumveka bwino mau polankhula, koma anthu ndi ziwan-da zonse zinalephera kupeka mau angati a mu Qur’an imeneyi yolemekezekayi. Uwu ndi umboni woti Quru’an imeneyi inachokera kwa Mulugu (152).

Ndithu Mulungu wapamwamba mwamba amapanga zomwe akufuna, ndipo amakhala ndizolinga za nzeru zakuya, zina mwa izo timazidziwa ndipo zina sitimazidziwa, koma maumboni omveka akuonetsa poyera kuti mabuku akalewo sadali chozizwitsa, choncho sichidali chofunika kuti apitilire, komanso iwo anali malamulo anthawi yochepa ndi kwa anthu ochepa (153).

Funso ngati ili nthawi zambiri omwe amakonda kufunsa ndiomwe ali a msinkhu woyambira pakatikati ndikumapita mtsogolo, kotero tidzayenera kumulongosolera modekha ndi momuunikira mwanzeru zomwe zingatsindike kuti Qur’an ndi yoona, kenako timuuze kuti: ndithu zinthu zikanenedwa mobwerezabwereza ndikuchitika kambirimbiri zimakhazikika ndipo zikafala zimatsimikizika, ndipo Qur’an inatipeza kudzera munjira yofala (yowanda), ndipo timulongosolere tanthaunzo lakufalako ( التواتر ) kuti ndikulandilidwa nkhani ndi gulu lochuluka kuchokeranso ku gulu lochuluka losatheka kumveka ndi bodza, adziwe zimenezo anthu wamba ngakhalenso anthu odzitsata, ndipo asilamu anatengera zolandila nkhani zimenezi m’bado kuchokera ku m’bado wina, amaphunzitsana Qur’an imeneyi mokhala mwawo, amaiwerenga m’mapemphero awo, ndipo amawaphunzitsanso ana awo, moti titati tiyerekeze kuti munthu wophunzira wamkulu ndi wolemekezeka kwambiri komanso woopsa atati alakwitse chilembo chamu Quru’an mo, ana adzamudzudzula iye akulu akulu asanamudzudzule, choncho kufikira inatipeza ife Quran imeneyi ilibe choonjezera kapena chopunguka, ili yotetezeka yosasindidwa.

Atati atsuste mwanayo umboni umenewu ndiye kuti adzathanso kutsutsa maumboni ena onse omwe ali okhazikika ndi oona, monga kupezeka kwa mtumiki, ophunzira amtumiki (maswahaba) ndi anthu ena odziwika mumbiri yachisilamu, zoterezi ngakhale anthu anzeru onse sangagwirizane nazo (zotsutsa umboni umenewuzi), ndipo mu Qur’an Mulungu adawatchalenja anthu ndi ziwanda kuti abweretse chofanana ndi Qur’an yo ndipo sanakwanitse, ndipo mu Qur’an yonse mulibemo kusemphana kapena kukhulana ngakhalenso kupelewera ndipo kudabwitsika kwa nkhani zake, malamulo ndi mau ake ……. Zikusonyeza kuti ndithudi Qur’an yo sidachokere kwa munthu, chifukwa munthu ntchito zake komanso mau ake amasintha sintha komanso kupunguka; Qur’an yo inachokera kwa Mulungu ndipo iye anatenga yekha udindo woyiteteza (154).

MAFUNSO

OKHUDZA ATUMIKI

Iwo ndi anthu ochokeranso mwa ana a Adam, Mulungu anavumbulutsa kwa iwo utumiki ndipo anawalamula kufalitsa uthenga wa Mulungu kwa anthu awo, ndikuwaitanira kuti adzimupembedza Mulungu yekha. Mneneri woyamba ndi Adam ndipo womaliza wawo ndi Muhammad (saw). Chiwerengero chawo ndi chochuluka kwambiri chifukwa Mulungu amawatumiza iwo ku mibadwo yonse yomwe idapezeka padziko lapansili, moti nyengo iliyonse mumbiri zakale imakhala ndi mneneri wowaitanira anthu ake ndikuwaongolera kunjira yoongoka.

Mulungu adatumiza atumiki chifukwa cha chifundo chake pa anthu ndi kufuna kuwaongola, kuti (atumikiwo) afalitse kwa anthuwo uthenga wa mbuye wawo, ndiye mtumiki amakhala munthu yemwe anthu ake amamudziwitsitsa bwinobwino komanso yemwe iwo amaikira umboni za ubwino wake kuyambira asanalandire chibvumbulutso, ndipo Mulungu adawapanga atumiki kukhala chitsanzo chooneka ndi maso pa anthu, amawaphunzitsa iwo kudzera mmakhalidwe ndi zichitochito ndikumawalongosolera zomwe zingamawathandize ndikuwatalikitsira zomwe zingawazunze, moti kutumiza atumiki kunali kuika umboni pazolengedwa zake ndikuwasonkhanitsa anthu pachipembedzo chimodzi chomupembedza Mulungu yekha (155), chifukwa anthu akufunikira wowaongolera kunjira yoona muchilankhulo chawo, pachifukwa ichi Mulungu amavumbulutsa kwa atumiki amenewa mabuku muchiyankhulo cha anthu awo ndicholinga choti uthengawo uwapeze momveka bwino kwambiri.

Anenerinso ndi anthu mwaiwo mulinso matanthauzo aumunthu, Mulungu anawateteza iwo kumbali ya utumiki yokhayo, anawateteza kuti asagwere mu zomwe zingadetse zochita zawo kapena makhalidwe awo, ndicholinga choti akakhale chitsanzo chabwino, anthunso azikhutitsidwa ndi mau komanso zochita zawo, ndinso kuti chisakhale chifukwa chodetsera ntchito yawo yakufalitsa uthenga wa Mulungu, koma ngakhale zili choncho iwo ndi anthunso amatha kulakwitsa kwa wamba kosapereka vuto kuutumiki wawo, monga: kulakwitsa kuyeza malo oyenera kulima kapena a nkhondo, kapena mulingo wachidwi choyitanira anthu kuchipembedzo (156).

Iye ndi mneneri womaliza mwa aneneri omwe Mulungu anawatumiza kwa akapolo ake, ndipo dzina lake ndi Muhammad mwana wa Abdullah mwana wa Abdul-muttalib wochokera mwa Hashim wafuko la chiquraish, anabadwira ku makkah, tsiku lolemba mwezi wa Rabiul-awwal, chaka cha Njovu, bambo ake anamwalira iye ali m’mimba mwa mayi ake, mayi ake adamwalira iye ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi (6) zakubadwa, kenako analeredwa ndi agogo ake Abdul- muttalib omwe anadzamwalira mtumiki ali ndi zaka zisanu ndi zitatu (8), kenako anamulera iye amalume ake (bambo ake ang’ono) Abu Taalib, mtumikiyu ankatchedwa “wonena zoona wokhulupilika” chifukwa chakhalidwe lake lapa mwamba, analandira utumiki ali ndi zaka makumi anayi, anakhala akuitanira anthu ake kuchisilamu ku Makkah kwa zaka khumi ndi zitatu (13), kenako anthu aja atamuzunza kwambiri iye anasamukira ku Madina nakakhazikika kumeneko kwazaka khumi, analumikiza kumeneko ubale pakati pa asilamu ochokera ku Makkah ndi aku Madinako, Ndipo anakhazikitsa kumeneko malamulo a Mulungu, ndipo adamwalira kumeneko muchaka cha khumi ndi chimodzi chisamukireni kuchokera kuMakkah, komanso pambuyo pofalitsa uthenga wa Mulungu mokwanira ndikubweza kwa anuwake zonse zomwe anasungitsidwa (157).

Maumboni osonyeza kuti Muhammad ndi mtumiki ndi ambirimbiri, ndipo ofunikira kwambiri mwa iwo ndi: Quran yolemekezeka, buku limeneli ndi lozizwitsa zedi ndipo lakhala likudabwitsa mibado pambuyo pa mibado chifukwa cha nfundo za pamwamba zomwe zimagwedeza nzeru za anthu.
Chinanso chimene chimasonyeza za utumiki wake (SAW) ndi mbiri ya khalidwe lake yomwe adamusimba nayo adani ake asanamusimbe nayo omukonda ake, moti ankamutcha kuti “wonena zoona wokhulupirika”.
Umboni winanso ndi zozizwitsa zomwe aliyense amazidziwa zomwe anthu a nthawi yake adaziona, ndipo mibado ya m’mbuyo idamva kuchokera ku mibado ya kale.
Umboninso wina ndi malamulo ogwira mtima, ogwirana bwino, okoma komanso okwanira omwe ali mu chipembedzo cha chisilamu.
Umboni wina ndi nkhani zabwino zolosera za kubwera kwa iyezochuluka zomwe zikupezeka mmabuku akale.
Enanso mwa maumboniwa ndi kufalikira kosalekeza kwa chipembedzo cha chisilamu kumeneku pa malo aliwonse ndi nthawi zonse.
Ndipo umboni wina ndikufotokoza kwake mtumikiyu zokhudza mibado yakale ndi zinthu za mtsogolo (158).

Ndithu mtumiki (SAW) anayendesedwa kuchokera ku makkah kukafika ku mzikiti wa ku Jerusalem pa Buraq (chinyama chokwera), kenako anakakwezedwa kupita ku mwamba motsogozedwa ndi Jibril (Gabriel), ndipo Mulungu ndi wakutha chilichonse, palibe chomwe chingamukanike pansi pano ngakhalenso kumwamba, monga mmene tikuonera lero: amakwanitsa bwanji munthu wofooka kugwiritsa ntchito nzeru zake kupanga ndege yoyenda mwachangu kuposa mau, komanso anapanga chipangizo chojambulira zithunzizomwe zimampangitsa munthu kumaoneka wochuluka ndi malo angapo nthawi imodzi, ndiye Mulungu ndi wamkulu kwambiri yemwe ali ndi kuthekera kwakukulu kuposa zolengedwa zake.

Ndithu kutumizidwa kwa aneneri kumalumikizana ndi cholinga- kumene kuli kuongola ndi kuongolera- ndipo kukupezeka kuti mabuku akale anakumana ndi kusintha ndi kupunguka (ma chapter ndi ma verse ena) pambuyo pomwalira atumiki awo. Mulungu anachiona kuti ndi chanzeru zakuya kuti atumize mneneri ndi buku lomwe silingakumane ndi m’pungwepungwe ngati umenewu (kusintha ndi kupunguka), ndipo Mulungu anatenga udindo woliteteza kufikira tsiku lomaliza, ndipo poona kudabwitsa kwa Qur’an koti ilo ndi buku lomveka bwino lokhala ndi maumboni opambana pa zolengedwa zonse- mpaka kale kale, chinali chanzeru kuti mtumiki Muhammad (saw) akhale womaliza mwa aneneri ndi atumiki.

Chifukwa chakuti kumukonda iye ndi imodzi mwa nsanamira zachikhulupiliro, ndipo kukhulupilira mwa Mulungu sikungakhale kokwanira pokha pokha chikondi ichi chitapezeka, ndipo kumukonda Mulungu kumalumikizana ndi kumukonda onse kuti agwire ntchito yaikulu kwambiri ya utumiki imeneyi, chifukwa Mulungu anasankha munthu yemwe ali ndi khalidwe, mau ndi ntchito zabwino kwambiri komanso wochokera ku banja labwino kwambiri, chifukwa iye (Allah) ndi amene amamudziwa bwino munthu woyenera kumpatsa utumiki umenewu, ndipo poona kuti Mulungu ndi amene adamusankha iye pakati pa anthu onse pompatsa udindo waukulu umeneu.
Ndithu ndizoyenera kwa ife kumukonda kwambiri iyeyo kuposa munthu wina aliyense; chifukwa iye ndi amene anawadziwitsa za mbuye wawo, ndipo anali mneneri wabwino kwambiri kwa anthu ake, palibe mwazolengedwa ndi m’modzi yemwe amene anatipangira zabwino zapamwamba woposa iye (saw) (159), iye adapilira ndi mazunzo omwe amapezana nawo pa nthawi yoitanira anthu kuchipembedzo ndi ubwino, moti amabanika ndi kudandaula akamapanda kukhulupilira yemwe iye akumuitanirayo; chifukwa chowadandaulira zokalowa kumoto, Mulungu akunena kuti: “Mwina uziononga wekha pakuwadandaulira (anthuwo) chikhalidwe chawo kuti sakukhulupilira nkhani iyi,(Iyayi usakhale wodandaula ndi zimenezo)” (Surat Al kahaf: 6). Pachifukwa chimenechi mtumiki (saw) ndi amene ali woyenera kumukondetsetsa pambuyo pa Mulungu.

MAFUNSO

OKHUDZA KUKHULUPILIRA TSIKU LOMALIZA

Ilo ndi tsiku lomwe Mulungu adzaukitse zolengedwa zonse kuti akaziwerengere ntchito zake, ndipo limatchedwa lomaliza chifukwa palibenso tsiku lina pambuyo pake, ndipo limatchedwanso kuti ndi tsiku lamalipiro chifukwa Mulungu akawalipira anthu patsiku limeneli pa zintchito zomwe adatsogoza ali padziko lapansi lino, kotero yemwe angagwire ntchito yabwino kapena yomvera Mulungu ndiye kuti Mulungu akamulowetsa iye ku Jannah, ndipo yemwe angagwire ntchito zoipa nanyozera malamulo a Mulungu; Mulungu akamulowetsa iye ku moto, ndipo ili ndi tsiku lomwe lidzakhale lomaliza paumoyo wa padziko lapansi ndi kwa anthu onse. Tsikuli limatchedwanso kuti louka, kutanthauza kuti: patsiku limeneli anthu adzauka m’manda kulunjika kumwamba kuti akawerengeredwe ntchito zawo (160).

Palibe amene akudziwa kuti tsikuli lidzabwera liti, Mulungu akunena kuti: “Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuopa; (osati kulengeza za nthawi)” (Surat Annazi’ati: 45), Mulungu anatibisira tsiku limeneli ndi cholinga choti tilimbikire kugwira ntchito ndikukhala okonzekera tsiku lililonse, pogwira ntchito zabwino ndi kusiya ntchito zoipa; ndipo munthu akanadziwa tsiku limeneri lobwelera kwambuye wake sakanalapa kufikira nthawi itasala yochepa, ndipo dziko likanadzadza ndi zoipa kuposa m’mene liliri panopa (161).

Uku ndi kusonkhanitsa komwe Mulungu adzasonkhanitse anthu onse oyambilira mpakana omalizira, Mulungu akunena kuti: “Nena kwa iwo (poyankha kutsutsa kwawo) kuti ndithu, amibadwo yoyamba ndi yomaliza omwe inu muli m’gulu lawo adzasonkhanitsidwa m’nthawi ya tsiku lomwe lakhazikitsidwa” (Surat Al Waqi’ah: 49-50), nawaonetsa ntchito zawo ndikuwalipira molingana ndi momwe anagwilira ntchitozo, munthu yemwe angagwire ntchito yabwino akalipidwanso zabwino, ndipo yemwe angagwire ntchito yoipa adzalipidwanso zoipa, Mulungu akunena kuti: “ Choncho amene angachite chabwino cholemera ngati kanjere kakang’ono azaona malipiro ake, ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono, azaona malipiro ake” (Surat Azilizaal: 7-8).

Ndithu mwana wazaka zisanu ndi chimodzi ndikumatsika – nthawi zambiri- sangathe kumvetsa tanthauzo leni leni lainfa ndi kuuka kwa akufa.Komano zoona zake ndizoti infa ndi mathero eni eni amunthu wina aliyense pa umoyo uno, pomwe mwana wazaka zisanu ndi chimodzi kufikira wazaka zisanu ndi zitatu angathe kumvetsa nthawi zambiri- tanthauzo lainfa komanso zoti idzakhudza anthu onse, ndipo mwana woyambira zaka zisanu ndi zitatu kufikira zaka khumi; angathe kumvetsa mokwanira nkhani ya ifa ndikuuka kwa akufa, amatha kuona kapena kumva nthawi zina amatha kudutsana ndi nyengo ya infa m’banja mwake, nakhala kuti kumemeko ndikukumana kwake koyamba ndi infa, koma sitikudziwa m’mene angadzamvere kapena adzakhuzidwire akadzamva za infa ndi manda, zachidziwikire adzadzadzidwa ndi mantha chifukwa chakutchulidwa zinthu zimemezi; choncho tikuyenra kumulongosolera mwana za infa mosamunamiza komanso mogwira mtima mpaka akhutitsidwe kuti munthu womwalira amakhala kuti, ali paulendo- mwachitsanzo- munjira imeneyi mwana adzadziwa zenizeni kuchokera kwa anthu ena mwachangu.

Ndipo ndi bwino- mwana asanakumane ndi banja lomwe lili munyengo ya infa timudziwitse kapena timuonetse mbalame yakufa kapena mtengo wakufa, chifukwa zimenezi zidzamuwalitsira tanthaunzo la ifa mwa njira yokhudzika, kenako tiyetsetse kumulongosolera mwanayo mwachidule kuti ndithu munthu akamwalira amapita kukakhala mu umoyo wina, ndipo tonse tidzamwalira ndipo tidzakakumana ndi onse omwe adamwalira ndi kukhala nawo ku mtendere Mulungu akadzalora. Ndipo ndizofunika kuti mwana adziwe kuti ndithu infa simathero amunthu ayi, koma kuti ndi kusuntha kuchoka kwa munthu wokhulupilira kunka ku umoyo wabwino ndiwapamwamba kwambiri, komanso kusuntha kwa munthu woipa kukakumana ndi malipiliro azoipa, ndipo Mulungu akamatenga moyo wathu (kutipha) sizimatanthauza kuti Mulungu samatikonda ayi, koma amatenga moyo umeneu ndicholinga choti tikakhale naye pafupi m’minda yapamwamba komanso yokongola kwambiri yomwe kukongola kwake sitingathe kukuyerekeza (162).

Ana nthawi zambiri sapanga zoipa, ndipo salakwitsa mwadala, pachifukwa chimenechi; Mulungu amawalandira iwo mwachifundo nawalowetsa ku Jannah, ndipo munthu akamwalira naola,ndithu mzimu wake umakhalabe moyo chifukwa umakwera kupita kwa mlengi wake, ndipo mbiri ndi ntchito zake zabwino zimatsalirabe mmitima ya anthu, choncho, ndithu munthu akuyenera kukonzekera kukakumana ndi mbuye wake popanga zabwino ndi kugwiritsa ntchito maphunziro ndi malamulo a chisilamu (163).

Nthawi yathu yomwe Mulungu anatiikira kuti tikhale pa dziko pano ikatha; timasuntha kupita kumanda- awa ndi malo okhala akufa okhaokha-, ndipo mandawa atha kukhala bwalo mmabwalo aku Jannah kwa munthu yemwe angakhulupirire mwa mbuye wake, kumumvera malamulo ake , ndikugwira ntchito zabwino pamene ali moyo pa dziko la pansi, adzasangalala mmandamo kufikira tsiku louka kwa akufa (164).

Inde wakufa amamva salaam tikamawapatsa, amawafikanso mapemphero anthu tikawapemphelera, koma sapuma ngati ife ayi chifukwa iwo samafunikira kupuma, chifukwa iwo ali moyo wina wosiyana ndi moyo wathu wadziko lapansiwu, choncho; moyo umene uli nkudza umayambira m’manda, umakhala ndi dongosolo lake lake ndi chibadwa chake chake chosiyana ndi moyo uno, kulibe kupuma, kudya, kumwa, kugona ngakhale kugwira ntchito zina, koma kusangalala kwa mpaka kale kale, kapena zilango zampaka kale kale (165).

Jannah ndi nyumba ya mtendere, ndi malo okongola komanso kuli chilichonse chimene umachilaka laka ndi chomwe umachikonda. Jannah ndi malo omwe amapita anthu olungama omwe amamgwira ntchito yabwino, Jannah ili ndi makomo asanu ndi atatu (8) komanso osanjikizana opita m’mwamba, azikalowa anthu okhulupilira molingana ndi mulingo wa ntchito zake zabwino ndi chifundo cha Mulungu pa iye, yemwe adzakhale ndi ntchito zabwino zochulukitsitsa adzakhalanso pamalo okongoletsetsa ndi apamwamba kwambiri kuposa wa ntchito zochepa, komabe onse adzakhala osangalala, okondwera komanso moyo wa mtendere, mu Jannah tizikahalamo osangalala, sitidzadwala ngakhale kutopa, tikamuonako Mulungu, mtumiki (saw) ndi aneneri onse kuphatikizapo ndi onse amene timawakonda- Mulungu akadzalola-, kumeneko kuli chilichonse chimene tingachikonde ndi kuchifuna, kuchokera muchakudya ndi chakumwa, chisangalalo ndimitendere (166).

Moto ndi nyumba kapena malo azilango, ndipo ndi malo omwe Mulungu anawakonza ndi cholinga choti akawalangiremo onse ogwira ntchito zoipa kapena kuzunziramo anthu onyozera Mulungu, omwe samamvera malamulo ake.

Zinyama sizinalamulidwe malamulo, koma izo ndi zolengedwa zomwe Mulungu adazipeputsa kuti zitumikire anthu, moti izo sizidzawerengedwa kapena kulangidwa ayi, tsiku lachiweruzo Mulungu adzazisonkhanitsa zinyama zonse naziuza kuti zibwezerane zina ndi zinzake zomwe zidalakwirana padziko lapansi, moti mbuzi yopanda nyanga adzaiuza kuti ibwezere ku yanyanga yomwe inaibaya iyo, Mulungu akadzamaliza kuzilamulira zinyamazo kubwezeranako adzazilamula kuti zisanduke dothi! ndipo zidzatero (167).

MAFUNSO

OKHUDZA KUKHULUPILIRA CHIKHONZERO CHA MULUNGU

Zonzse ziwirizo ndi imodzi mwa msanamira za chikhulupiliro Mulungu akunena kuti: “Ndipo adalenga chilichonse ndikuchilinga mulingo wake” (Surat Al Furuqan: 2) ndipo tanthauzo lachigamulo ndi chikonzero ndiko kuti Mulungu m’mene anadziwa mmene zinthu zidzakhalire mtsogolo monse zisanapezeke zinthuzo, kapena kulembedwa asadafune kuzilemba komanso asanazilenge (168).

Nzotheka kumuuza chitsanzo chokhuzika komanso chophweka choti: yemwe anapanga masewero (ma game) omwe iye amasewera, amadziwa zomwe gemuyo ingathe kuchita zisanachitike; chifukwa iye ndi amene anaipanga naiikira chilichonse chachikulu ndi chaching’ono chammenemo ntchito yake yomwechizigwira. Ndipo iye amazindikira kotheratu kuthekera kwa gemu imeneyi ndi mbali zomwe izitha kuyambira kapena kugwedezeka ikamagwira ntchito. Ndiye Mulungu ndi amene anamulenga munthu ameneyu yemwe akutha kupanga ma gemu amenewa, choncho Mulungu ndi amene ali ndi kuthekera ndi kuzindikira koposa komanso ndi amene ali wokhonza mokwanira, ndipo iye anachizindik-ira kotheratu chilengedwe chilichonse asanachilenge, pamene amalenga, ndi pambuyo pochilenga. Ndipo Mulungu ndi amene analenga munthu, nyengo ndi malo, komanso iye amadziwa zomwe zinalipo kale, zomwe zikupezeka nthawi ino, ndi zomwe zidzachitike ntsogolo zisanachitike.

Ndithu munthu amakakamizidwa pa zinthu zina, tonsefe timakakamizidwa ndipo tilibe kusankha pa zinthu monga: kubeleka, kufa, nyengo yokhala moyo, sitimadzisankhiranso makolo, timakakamizidwanso kulumikiza ubale (kusadula ubale). Ngakhale zili choncho komabe tinapatsidwa kusankha pazinthu zina monga; kupemphera kapena kusapemphera (kuswali kapena ayi), kukhulupilira kapena kusankhulupilira ngakhalenso kusankhako kuli choncho; ndithu chifuniro chathu chimakhala mkati mwa chifuniro cha Mulungu; izi zikutanthauza kuti Mulungu akanafuna kuti asatipatse ufulu wosankha akanatha kutero, ndipo akanafuna kutiletsa kapena kukana akanatha kutero. Koma iye anapereka ufulu wosankha kwa munthu kenako akamuwerengere pachisankho chakecho, ilo ndi tanthauzo la Mulungu lonena kuti: “ Ndipo simungafune chithu mwainu nokha pokha pokha atafuna Mulungu mbuye wa zolengedwa zonse” (Surat Attakweer: 29) ndipo tithe kumulongosolera mwanayo tanthauzo la kukakamizidwa ndi kusankha kumeneku, kudzera mu zichitochito, mwachitsanzo mphunzitsi abweretse kapu ya galasi (tambula) ndiye amufunse mwanayo kuti: kodi ungathe kuiponya tambula imeneyi pansi kuti isweke? Zachidziwikireni kuti mwana azayankha kuti: inde ndingakwanitse, kenako mphunzitsiyo amupatse mwanayo tambulayo kuti aiswe, apa mwana uja sadzafuna kuphwanya tambulayo, ndipo mphunzitsi azailandire tambulayo kuchokera kwa mwanayo namufunsa iye kuti chifukwa chiyani sunaiswe tambulayi? Iye adzati kuphwanya tambulayo n’kulakwitsa, sizoyenera kuchita zimenezo,apa mphunzitsi avomereze ndi kuonjezera mau ponena kuti: ndithu Mulungu anadziwa kale kuti iwe sungadzaiswe tambula imeneyi, chifukwa ndiwe mwana wabwino, anadziwanso kale kuti mwana woipa adzaiswa.

Nanga iweyo alipo amene wakuletsa kuiponya tambula imeneyi pansi, kapena pali yemwe akanamukakamiza mwana woipa kuti aiswe tambulayi? M’menemo ndi m’mene chimakhalira chiongoko ndi kusochera. Kenako auzidwe mwanayo kuti: ndithu munthu sadziwa zomwe Mulungu adamulengera, iwenso supemphedwa kuti udziwe zomwe adakulembera, chomwe ukupemphedwa kuchita ndi kukhulupilira kuti kuzindikira kwa Mulungu ndikokwanira ndipo kulibe malire.
Chimodzi modzi kulembedwa kwa zikhonzero: iwe umangofusidwa zachifuniro chako ndi mulingo wako wakutsatira kwako malamulo ndikusiya kwako zoletsedwa, izi zimakhala zochokera mukuthekera kwako ndi chifuniro chako (169).

Mulungu adaongola anthu onse, potengera mau a Mulungu onena kuti: “Ndipo tamulongosolera njira ziwiri: (yabwino ndi yoyipa, ndipo tampatsa mpamvu yosankhira njira yomwe akafuna)” (Surat Al Balad: 10),ndipo tanthauzo lachiongoko lomwelili muvesili ndi chiongoko chomufotokozera munthu momveka njira yolungama kuti choonadi chikhale choonekera, komanso bodza lionekere poyera kuti ndi bodza. Mulungu adawasiyira anthu ufulu wosankha, ena amasankha njira yabwino (yoona) pomwe ena amasankha njira yoipa (170).

Kudziwa uku ndi kwa Mulungu yekha, munthu sadziwa zimenezi,munthu amangoganizira mwaumbuli. Choncho; munthu adzawerengedwa pa ntchito zomwe wagwira pa umoyo wadziko lapansi pano. Ndipo kapolo wa Mulungu sangakwanitse kudziwa zobisika zomwe Mulungu adamulengera iye mpaka atachichita kapena kumupeza. Ndiye chikonzero chomwe chinalembedwa ndi umboni wa chomwe chachitika osati wa chomwe sichinachitike ayi. Komanso afunsidwe mwanayo kuti: ndithu Mulungu adakulembera zinthu za dziko la pansi… nanga nchifukwa ninji iwe umapanga zokhazo zimene zingakuthandize ndikumasiya zomwe zingakupatse mavuto? Tingathenso kumpatsa chitsanzo choti: munthu atafuna kupita dziko lina lake lomwe lili ndi njira ziwiri; imodzi mwa njirazi ndiyosaopsa pomwe inayi ili ndi chiopsezo, kodi munthu angasankhe njira yanji pa njira ziwirizi? Mosakaikitsa iye adzasankha njira yosaopsayi, chimodzimodzinso popita ku umoyo womwe uli nkudza munthu amasankha njira yachitetezo kuti akafike ku Jannah – njira imeneyi ndiyo kutsatira malamulo ndi kusiya zoletsedwa- , zikadakhala kuti chikonzero ndi umboni wa aliyense, sitikadakwanitsa kuwagwira olakwa ( criminals), chifukwa iwo akadapereka umboni woti iwo achita zimenezi chifukwa cha chikonzero (171), choncho munthu akuyenera kusangalatsidwa ndi chikonzero ndikuzisiya mmanja mwa Mulungu wapamwambamwamba , chifukwa Mulungu “ Safunsidwa pazimene akuchita koma iwo (anthuwo adzafunsidwa” ( Surat Al-Anibiyay:23), zolengedwa zonse ndi zake ndipo malamulo onse ndi ake ndipo iye ndi mwini kulamula.

Mulungu akunena kuti: “Sindidalenge ziwanda ndi anthu koma kuti azindipembedza” (Surat Adhariat: 56), pindulira ife tomwe- kumupembedza iye-, ndipo anayika zotsatira zake kuti lidzakhale tsiku lomaliza molingana ndi ntchito zathu, Jannah kwa olungama ndipo moto kwa ochimwa. Ndipo dziko lonseli ( الكون ) ndi cholengedwa cha Mulungu, ilo linalengedwa mwaluso ndi mwanzeru zakuya, analenga mitambo ndi nthaka, anaikamonso m’menemo maiko (planets), analenganso nyenyezi, kukhala zizindikiro, phunziro, ndi zikongoletso zadzikoli, ndipo analenga dzuwa kuti lidzitipatsa kutentha, kuotcha komanso kuthandizira kumeretsa mbeu ndi kupha tizilombo toyambitsa matenda (germs), ndipo adalenga zinyama kuti zitumikire anthu, azizidya, kuzikwera kapena kunyamulira katundu wawo, Mulungu akunena kuti: “Adalenganso ngamila, nyumbu ndi abulu kuti muzizikwera ndikutinso zizikhala zolowetsa chisangalalo mmitima yanu ndipo adzalenga zokwera zina mtsogolo muno zomwe simukuzidziwa” (surat Annahal: 8), ndiye kulenga nthaka ndi zinthu zimenezi kunachitika munthu asanalengedwe, konseko ndikumulemekeza munthuyo mwapadera dera kuposa zolengedwa zina- ngakhale zolengedwa zina zonsezo zimamutamanda Mulngu, izonso pazokha zimapembedza Mulungu, Mulungu akunena kuti: “Ndipo palibe chilichonse (mwa zolengedwa) koma chikulemekeza ndi kutamanda Mulungu koma inu simuzindikira kulemekeza kwawo ndithu iye Mulungu ngodekha, ngokhululuka” (Surat Al Isra:44).

Iwo adzakakhala pakati pa kufunsidwa ndi kuwerengeredwa, chifukwa Mulungu adawapatsa iwo nzeru, ndiye Mulungu adzawayesa mayesero pa tsiku lachiweruziro ndikuwalamula, akadzayankha molondola ndikumvera akalowa ku Jannah, koma akadzanyozera adzalowa ku moto.

Dziko limeneli ndi malo a mayesero ndipo lili ngati gawo loyamba la nkhani yamagawo awiri, pomwe moyo uli nkudza ndi malo amalipiro ndikuwerengeredwa komanso kubweza opondereza zomwe adawapondereza oponderezedwa, ndipo tsiku lomalizali lili ngati gawo lachiwiri la nkhani ija, pachifukwa chimenechi ndithu kupezeka kwa anthu oipa ndikusawalanga kwawo pa dziko la pansi pano, amenewo ndi mayesero ndipo pa (moyo wa dziko lino ) umenewu simathero a zonse ayi, koma padzafunika kuuka kwa akufa tsiku lachiweruziro kuti aliyense akapeze malipiro antchito zake, Mulungu akunena kuti: “Choncho amene angachite chabwino cholemera ngati kanjere kakang’ono adzaona malipiro ake, ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono adzaona malipiro ake”. (Az-zilzaal: 7-8).

Ndithu Mulungu adalenga anthu ndikuwapatsa ufulu wosankha zabwino kapena zoipa. Iweyo ungathe kukhala wakhalidwe labwino kapena loipa, koma umayenera kuzilandira zotsatira zakhalidwe lako ndipo uwu ndi mtendere ndi nzeru zakuya zochokera kwa Mulungu; moti anthu oipa aja angakwanitse kukhala abwino,ndipo ntchito yathu ndi kuwathandizira chimenechi, akakana napitiliza kuipa, kudzakhala koyenera kwa ife kuwaletsa kuchitira zoipazo anthu ena , ndicholinga choti Mulungu atikonde ndikutilipira, ndipo Mulungu ndi amene analenga chilichonse mu umoyo uno, ndipo moyo uno ndi malo amayesero, Mulungu akunena kuti: “ Amene walenga infa ndi moyo kuti akuyeseni mayeso ndani mwainu ali wochita zabwino kwambiri” (Suratul-mulk:2), ndipo ena mwa mayesero amenewa ndi kupezeka kwa zoipa mmanja mwa satana ndi anthu osochera (174)

Iwo amakhala kuti Mulungu awayesa mayeso owapungula china chake kapena powapatsa matenda; ndi cholinga choti akapirira Mulungu akawaonjezere zabwino, komanso ndicholinga choti amene ali abwino athokoze mtendere womwe Mulungu wawapatsa powapanga ambiri mwa iwo kukhala alungalunga (opanda chilema) ndi athanzi (opanda matenda), kuti tizimuthokoza pa zimenezi, komanso ndicholinga chotikumbutsa kuchepera kwa kuthekera kwathu poyerekeza ndi kuthekera kwa Mulungu, kotero palibe chifukwa chodzitukumulira, koma tizidzichepetsa ndi kuthandizana wina ndi mzake, ndipopa tsiku lowerengetsera: anthu opanga zabwino akakhala moyo wosatha ali athanzi (osadwala) mminda ya mtendere – mu chifuniro cha Mulungu (175).

Ndithu chuma chonse cha padziko lapansi chinachokera kwa Mulungu, ndipo Mulungu amawayesa akapolo ake, nthawi zina amawapatsa chuma anthu abwino kuti awayese ngati azithandiza anthu ena, ndipo nthawi zina amamumana chuma kuti amuyese m’mene angamapililire osaba kapena osapanga nsanje, ndiye nthawi zonse zomwe munthu wabwino ameneyu angakhale mu umoyo wochepaumenewu (wadziko lapansi) ali wopilira ikamupangitsa kupeza malipiro akulu kwambiri tsiku lowerengetsedwa, pomwe yemwe anapatsidwa chuma chambiri ndipo sanathandize anthu ena nazunza nacho anthu ena, adzakalangidwa tsiku louka kwa akufa; chifukwa iye sanathokoze mtendere wa Mulngu.

Tingathenso kumuuza kuti: ndithu Mulungu analenga anthu m’magulu osiyana siyana olemera ndi osauka; ndicholinga choti olemera achitire chifundo osauka, ndipo amphamvu athandize ofooka, Mulungu ali ndi cholinga chapamwamba powasiyanitsa anthu pa chili chonse, zilankhulo zawo ndi zosiyana siyana chimodzimodzinso mitundu yawo, mafuko ndi zibadwa zawo ndi zosiyana, ena ndi otakataka pomwe ena ndi aulesi ena amatha kutengera za anzawo pomwe ena ndiofuna zawo zokha, ena opereka ndipo ena ndi aumbombo, amasiyananso pachuma ndi zinthu zina zomwe ali nazo, ena ndi olemera ndipo ena ndi osauka, koma onsewo ndi mayesero, kulemera ndi mayesero ndipo kusaukanso ndi mayesero; amamuyesa wolemera kuti kodi athandiza anthu ena? Adzapereka chopereka chapa chaka (zakah)? Adzapereka chopereka chaulere chanthawi ina iliyonse (sadaka)? Ndipo amamuyesa wosauka kuti kodi apilira? alimbikira kugwira ntchito? Aziyenda yenda dziko lapansi kufuna funa chuma (mariziq)? Kapena azipanga ziphuphu (katangale)? Kapena azikhalira kuba?

Onsewa ndi mayesero, koma chitsimikizo chokalowa kumtendere chili pa onse; ndithu chuma chimachokera kwa Mulungu, ndipo kulemera ndi kusauka sikumalepheretsa kukalowa ku Jannah kapena kumoto, ndipo aliyense amalamulidwa molingana ndizomwe ali nazo ndipo anthu onse anakakhala olemera, sakanapezeka womugwilira ntchito nzake, ndipo palibe yemwe akanafuna thandizo kuchokera kwa nzake, Mulungu akunena kuti: “ Ndicholinga choti ena mwaiwo awachite anzawo kukhala antchito awo” (surat Azuhulf: 32), kutanthauza kuti aziwalirana( azitumikira ena kwa anzawo) wina ndi nzake, umu ndi mmene theyara la moyo uno limayendera koma kuti anthu onse akhale ofanana, ndiye kuti umoyo utha kuima (176).

Mulungu amakhala akumuyesa munthu wina aliyense kuti kodi apilira kapena akwiya? Ndipo Mulungu amamulipira munthu wopilira malipiro aakulu zedi, munthu wokhulupilira adzasangalala ndi malipiro amenewa patsiku louka kwa akufa, ndiye matenda, mavuto ndi zowawa, zonsezo ndi zikonzero zomwe Mulungu adayika kuti akwezere masitepe a anthu ndikuyeretsera mitima ndi zikhalidwe zathu kuti tisakhale odzimva ndi odzikweza, ndipo m’menemo ndimomwe wokhulupilira amadziyandikitsira kwa mbuye wake pomupempha komanso popilira,ndipo chikhulupiliro chake ndi zabwino zake zimaonjezereka,komanso Mulungu amamukonda, komanso (amatiyesa) kuti munthu aphunzire kufunika kwa thanzi ndi mitendere ina yomwe Mulungu amatipatsa.

Tingathenso kumupatsa chitsanzo cha galimoto, timufunsa iye kuti: kodi chifukwa chiyani idapangidwa galimoto? Kuti iziyenda, si choncho? Nanga nchifukwa chiyani kampani imene idapanga galimoto imeneyi inayika mu galimotomo ma bureki? Kodi zimenezi sizimatsutsana ndi kuyenda kwakeko? Ndithu kugwiritsa ntchito ma bureki ndi kofunikira ndi cholinga chofuna kusamala galimotoyo, galimoto inapangidwa kuti iziyenda pomwe ma bureki kuti iziima (isamayende) pa nthawi yoyenera kuti isamuvulaze mwiniwakeyo, ngakhale Mulungu anatilenga kuti tizisangalala popembedza iye komanso tizisangalala ndi mitendere yomwe iye anatipatsa.
Komabe analenganso mavuto kuti azimukumbutsa munthu wa chibwana komanso wotailira chintchito chake chachikulu chomwe Mulungu adamulengera,kotero asiye kutailira ndi kuiwala kwakeko, ayambe kumukumbukira Mulungu pomupempha chikhululuko, kupirira ndikukhala ndi chiyembekezo mwa Mulungu (177).

Mulungu ndi mlengi komanso mbuye wa chili chonse , Mulungu adalenga izo mukuthekera kwake komanso ndi cholinga cha nzeru za pamwamba; chifukwa Mulungu ndi wanzeru zakuya komanso ndi wozindikira, amadziwa zokhudza zinyama zimenezi zomwe ife sitidziwa; chifukwa kudziwa ndi kuzindikira kwathu komwe Mulungu anatipatsa ndi kwapang’ono zedi poyerekeza ndi kudziwa komanso kuzindikira kwa Mulungu, pa chifukwa chimenechi Mulungu akunena kuti: “Ndipo inu simunapatsidwe nzeru (zozindikira zinthu) koma pang’ono chabe”. (surat Israai: 85),ndiye ife sitingathe kudziwa zolinga zonse zomwe Mulungu analengera zinyama zimenezi,komabe zina mwa zolinga zimenezi ndi: kuonetsa ukadaulo wa Mulungu pa zolengedwa zake ndi kayendetsedwe kake ka zolengedwa zake,ngakhale zachulukitsitsa iye amazidyetsa zonsezo, chimodzimodzinso amatiyesera nazo mayesero ndikumulipira yemwe wazunzidwa ndi zinyama zimenezi, komanso zimaonetsa mphamvu zayemwe wapha zinyama zimenezi, ndipo zimaonetsa kufooka kwa munthu akamazunzika ndikudwala chifukwa cha cholengedwa chomwe ndi chaching’ono kwambiri poyerekeza ndi munthu. Ndipo kudzera muzachipatala ndi kafukufuku zapezeka kuti mankhwala ena amachokera ku poison wanjoka ndi zina zotero, komanso njoka zimadya mbewa (makoswe) zomwe zimaononga mbewu zakumunda, ndipo zina mwa zilombo zozunza zimenezi ndichakudya cha zinyam zina zaphindu, izi zikupanga tcheni (life cycle) cha moyo wa zolengedwa chomwe Mulungu adachilenga mwaukadaulo (178).

Ndithu mapemphero omwe Mulungu anatikakamiza ali ngati njira zoyeretsera mtima wa munthu ndi kutukulira mzimu wake kukhala wapamwamba. Licheperenji thukuta lomwe limakhetsedwa pochita mapempheroamenewa, poyerekeza ndi zabwino zomwe amapeza akatero (179). Ndiye pachifukwa chakuti mumapemphero (swalat) muli kuwerengedwa kwa Qur’an, kumutchula Mulungu (dhikiri) ndikumupempha Mulungu (dua), amasokhanitsa mapemphero amenewa (swalayi) mitundu yosiyana siyana ya mapemphero (ibadah) mokwanira, izizikupangitsa mapephero (swalat) kukhala opambana kuposa kuwerenga Quru’an pa kokha, ndikutchula Mulungu (dhikiri) pa kokha, komanso kumupempha Mulungu( dua) pa kokha. Zilichoncho chifukwa swalat imasonkhanitsa zonsezo kuonjezeranso pamapemphero a ziwalo (180) .

Ndithu anthu okhulupilira amasangalatsidwa ndi swala chifukwa iwo mu swalamo amakhala chifupi komanso akulankhulitsana ndi Mulungu, akumupempha zonse zomwe amazilaka laka, ndipo Mulungu ndikumayankha; ndipo ife timapemphera (swalah) chifukwa chakuti Mulungu anatilamulira kutero, ndipo ife nthawi zonse timafuna kumapanga zomwe Mulungu watilamula, ndipo timagwadira Mulungu chifukwa iye ndi amene anatilenga ndipo iye amatidyetsa, ndipo iye ndiye woyenera kupembedzedwa pachifukwa cha mitendere yosawerengeka yomwe watipatsa, Mulungu akunena kuti: “ Ngakhale mutawerengetsera mtendere wa Mulungu simungakwanitse kuwerengetsera yonse” (surat AN-nahali: 18), ndithu kupembedza kumeneku kuli ngati kuonetsa chikondi chathu ndikuthokoza kwathu kwa Mulungu, komanso kuonetsa kuti ife timafunikira thandizo la Mulungu, ndicholinga choti atisungire thanzi lathu ndi kutipatsa kuthekera kopanga zabwino ndikutichingira zoipa, pomwe Mulungu safunikira zimenezo, chifukwa iye ndi wolemera kwambiri safuna thandizo lathu ngakhale la ntchito yathu ndipo sizingamuthandize kathu.

Ndiye mapemphero ndi malamulo ochokera kwa Mulungu omwe iye anafuna kuti tizimupembedzera kudzera munjira yomwe anabweretsa mtumiki Muhammad (saw), ndipo ilo ndilo tanthauzo la maumboni awiri (shahadatain), kutanthauza kuti timamupembedza kudzera muchiphunzitso cha mneneri Muhammad, choncho chifukwa chakuti mapemphero amenewa ndi njira yathu yopezera malipiro aakulu omwe akatipangitse kukalowa ku Jannah, ndithu Mulungu anali ndicholinga cha pamwamba choti asakamupatse munthu wina aliyense malipiro pokha pokha agwire kaye ntchito, pachifukwa chimenechi, Jannah ndi katundu (malonda) wa Mulungu,- ndipo ngodula zedi-, kotero akufunikira kukhala ndi mtengo waukulu womwe uli kumvera (malamulo aMulungu) (181).

Ndithu pempho (dua) lili ndi miyambo yake yofunika kuitsatira ina mwaiyo ndi: wopempha alemekeze malamulo ndi chiphunzitso cha mtumiki pa dua kapena malamulo omwe Mulungu adaika oyendetsera dzikoli, ife timamupempha Mulugnu ndipo iye amatipangira zabwino kwambiri zomwe amatisankhira, nthawi zina umatha kuwapempha bambo ako kuti ukaseweretse njinga pa msewu wamagalimoto iwo ndi kukana; chifukwa iwo amakukonda kwambiri ndipo aona kuti kusakuvomera pempho lako ndizomwe zili zabwino kwambiri kwa iwe, ndiye malinga ndi kuolowa manja kwa Mulugu amaiika dua yathu pa imodzi mwanyengo zitatu: yoyamba: atha kutiyankha ndi kutitheketsera zomwe tapemphazo, yachiwiri: atha kutichotsera nayo (duayo) vuto kapena choipa china chake chomwe chikanatigwera, yachitatu: atha kutisungira chomwe tapemphacho kuti tikachipeze kapena chikatichitikire ku Jannah tsiku louka kwa akufa chinthu chabwino kwambiri kuposa chomwe tinapemphacho (182).

Chifukwa Mulungu adamulenga munthu wina aliyense m’maonekedwe osiyana ndi nzake, ndipo cholengedwa ndi Mulungu chili chonse ndi chokongola monga mmene Mulungu akunenera kuti “Palibe chikaiko, tamulenga munthu m’kalengedwe kabwino (kwambiri)” (surat tini: 4), ndiye munthu wina aliyense amadziwika potengera kalengedwe kake, moti yemwe Mulungu adamulenga kukhala wokongola kwambiri akuyenera kuthokoza kwambiri, ndipo yemwe Sali choncho akuyenera kusangalatsidwa nazo ndikuchilandila chimenechi, ndipo yemwe angathokonze ndiyemwe angapilire ali ndi ma sitepe ndi malipiro akulu zedi (183).

Ndithu Mulunguamatiyesa ndi cholinga choti asiyanitse pakati paanthuolungama ndi anthu oipitsa, Mulungu amatha kumuyesa munthu ndicholingachoti munthuyo azithawira kwa iye, ndi kudziyandikitsa kwa iye nthawi zonse, ndiye mayesero omwe Mulungu amawayesa nawo okondedwa ake, amakhala ndi cholinga chowaonetsera poyera kuti iwo amawakonda, ndi kuwakwezera ma sitepe awo ndikuti akhale chitsanzo cha ena; kuti nawonso azipilira ndikukhala ngati iwo, pachifukwa ichi mtumiki (saw) anati: “Anthu omwe amayesedwa mayesero kwambiri ndi atumiki kenako anthu olungama kwambiri kenako otsatira paiwo (pakulungama)” (Bukhar: -992), ndiye munthu amayesedwa molingana ndi sitepe yake (yomwe ali) pachipembedzo, akakhala wolimba pa-chipembedzo, Mulungu amamukhwimitsira mayesero, ichi ndi chifukwa chomwe Mulungu amawayesera aneneri maysero akulu kwambiri, ena mwaiwo mpaka anaphedwa, ena kuzunzidwa, ena kudwala kwambiri komanso nthawi yaitali monga: Ayyubu, ndipo mtumiki wathu Muhammad (saw) anazunzidwa ku Makkah ndi ku Madinah, komabe iye anapilira. Mfundo yaikulu pamenepa ndiyakuti mazunzo amabwera pa anthu okhulupilira ndi oopa Mulungu molingana ndikuopa kwawo Mulungu ndi chikhulupiliro chawo (184), ndipo zikuyenera kukhazikika mu mtima mwa mwana kuti: ndithu Mulungu amapanga zomwe wafuna, ndipo Mulungu safunsidwa pazochita zake, chifukwa iye ndi wolamula kuposa olamula onse.

Amenewa adali ambiri mwamafunso omwe amafunsidwa funsidwa, ndipo ife tikukulandirani kuti munthu akafuna kulumikizana nafe apeze ([email protected]) yathu kuchokera kwa sheikh wathu uyu (Adams Maxwell) pakafunika mayankho amafunso ena, kapena mukafuna kupereka zitsanzo zina zabwino kwambiri kuposa zimene tabweretsazi. .